2 Mbiri 2:4 - Buku Lopatulika4 Taonani, nditi ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, kumpatulira iyo, ndi kufukiza pamaso pake zonunkhira za fungo lokoma, ndiyo ya mkate woonekera wachikhalire, ndi ya nsembe zopsereza, m'mawa ndi madzulo, pamasabata, ndi pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika za Yehova Mulungu wathu. Ndiwo machitidwe osatha mu Israele. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Taonani, nditi ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, kumpatulira iyo, ndi kufukiza pamaso pake zonunkhira za fungo lokoma, ndiyo ya mkate woonekera wachikhalire, ndi ya nsembe zopsereza, m'mawa ndi madzulo, pamasabata, ndi pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika za Yehova Mulungu wathu. Ndiwo machitidwe osatha m'Israele. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Ineyo ndikufuna kuti ndimangire nyumba Chauta, Mulungu wanga, ndipo kuti ndiipereke kwa Iye, kuti ikhale yoperekeramo zofukiza za fungo lonunkhira bwino pamaso pa Mulungu, ndi yoperekeramo kosalekeza buledi wopatulika. M'nyumbamo aziperekeramonso nsembe zopsereza m'maŵa ndi madzulo, pa masiku a sabata, pa masiku okhala mwezi ndi pa masiku achikondwerero a Chauta, Mulungu wathu, potsata malamulo okhalira Aisraele mpaka muyaya. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Tsono ine ndikufuna kumanga Nyumba ya Yehova Mulungu wanga ndi kuyipereka kwa Iye kuti tiziyikamo buledi wopatulika nthawi zonse ndiponso kuperekeramo nsembe zopsereza mmawa uliwonse ndi madzulo ndi pa masabata ndi pa masiku a chikondwerero cha mwezi watsopano ndiponso pa masiku osankhika a chikondwerero cha Yehova Mulungu wathu, monga mwa malamulo a Aisraeli mpaka muyaya. Onani mutuwo |