2 Mbiri 2:3 - Buku Lopatulika3 Ndipo Solomoni anatumiza kwa Huramu mfumu ya Tiro, ndi kuti, Monga momwe munachitira Davide atate wanga, ndi kumtumizira mikungudza yommangira nyumba yokhalamo, mundichitire ine momwemo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ndipo Solomoni anatumiza kwa Huramu mfumu ya Tiro, ndi kuti, Monga momwe munachitira Davide atate wanga, ndi kumtumizira mikungudza yommangira nyumba yokhalamo, mundichitire ine momwemo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Adatumiza mau kwa Hiramu mfumu ya ku Tiro, adati, “Monga momwe munkachitira ndi Davide bambo wanga, pomamtumizira mitengo ya mkungudza, kuti amangire nyumba yake yoti azikhalamo, muchitenso momwemo ndi ine. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Solomoni anatumiza uthenga uwu kwa Hiramu mfumu ya ku Turo: “Munditumizire mitengo ya mkungudza monga munachitira ndi abambo anga pamene munawatumizira mitengo ya mkungudza yomangira nyumba yaufumu yokhalamo. Onani mutuwo |
Ndipo ataitsiriza, anabwera nazo ndalama zotsala kwa mfumu ndi Yehoyada, napanga nazo zipangizo za nyumba ya Yehova, zipangizo za kutumikira nazo, ndi kupereka nsembe nazo, ndi zipande, ndi zipangizo za golide ndi siliva. Ndipo anapereka kosalekeza nsembe zopsereza m'nyumba ya Yehova masiku onse a Yehoyada.