Numeri 28:9 - Buku Lopatulika9 Ndipo tsiku la Sabata anaankhosa awiri a chaka chimodzi, opanda chilema, ndi awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndi nsembe yake yothira; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Ndipo tsiku la Sabata anaankhosa awiri a chaka chimodzi, opanda chilema, ndi awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndi nsembe yake yothira; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 “Pa tsiku la Sabata muzipereka anaankhosa aŵiri amphongo a chaka chimodzi opanda chilema. Muziperekanso makilogaramu aŵiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ngati chopereka cha chakudya, ndipo muziperekanso chopereka cha chakumwa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 “ ‘Pa tsiku la Sabata, muzipereka nsembe ana ankhosa awiri a chaka chimodzi wopanda chilema, pamodzi ndi chopereka chachakumwa ndi chopereka chachakudya chokwana makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Onani mutuwo |
Taonani, nditi ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, kumpatulira iyo, ndi kufukiza pamaso pake zonunkhira za fungo lokoma, ndiyo ya mkate woonekera wachikhalire, ndi ya nsembe zopsereza, m'mawa ndi madzulo, pamasabata, ndi pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika za Yehova Mulungu wathu. Ndiwo machitidwe osatha mu Israele.