Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 28:8 - Buku Lopatulika

8 Ndi mwanawankhosa winayo umpereke madzulo; monga nsembe yaufa ya m'mawa, ndi nsembe yothira yake, umpereke; ndiyo nsembe yamoto ya fungo lokoma la Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndi mwanawankhosa winayo umpereke madzulo; monga nsembe yaufa ya m'mawa, ndi nsembe yothira yake, umpereke; ndiyo nsembe yamoto ya fungo lokoma la Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Mwanawankhosa wina uja muzimpereka madzulo, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa zonga zam'maŵa zija. Imeneyi ikhalenso nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Muzipereka mwana wankhosa winayo madzulo, pamodzi ndi chopereka chachakudya monga poyamba paja ndi chopereka chachakumwa monga mmawa. Ichi ndi chopereka chachakudya, fungo lokoma kwa Yehova.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 28:8
6 Mawu Ofanana  

Koma atsuke ndi madzi matumbo ndi miyendo; ndi wansembe abwere nazo zonse nazitenthe paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


nang'ambe mapiko ake osawachotsa konse ai; ndipo wansembeyo aitenthe paguwa la nsembe, pa nkhuni zili pamoto; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


koma atsuke ndi madzi matumbo ake ndi miyendo yake; ndi wansembe atenthe zonsezi paguwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Ndi nsembe yake yothira ya mwanawankhosa mmodziyo ndiyo limodzi la magawo anai la hini; m'malo opatulika uthirire Yehova nsembe yothira ya chakumwa cholimba.


Ndipo tsiku la Sabata anaankhosa awiri a chaka chimodzi, opanda chilema, ndi awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndi nsembe yake yothira;


ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa