Numeri 28:11 - Buku Lopatulika11 Ndipo poyamba miyezi yanu muzibwera nayo nsembe yopsereza ya Yehova: ng'ombe zamphongo ziwiri, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi opanda chilema; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Ndipo poyamba miyezi yanu muzibwera nayo nsembe yopsereza ya Yehova: ng'ombe zamphongo ziwiri, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi opanda chilema; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 “Pa tsiku loyamba la mwezi uliwonse, muzipereka nsembe yopsereza kwa Chauta. Nsembeyo ikhale ya anaang'ombe aŵiri amphongo, nkhosa imodzi yamphongo, anaankhosa asanu ndi aŵiri amphongo a chaka chimodzi, opanda chilema. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 “Pa tsiku loyamba la mwezi uliwonse muzipereka kwa Yehova nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa yayimuna imodzi, ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi, onse wopanda chilema. Onani mutuwo |
Taonani, nditi ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, kumpatulira iyo, ndi kufukiza pamaso pake zonunkhira za fungo lokoma, ndiyo ya mkate woonekera wachikhalire, ndi ya nsembe zopsereza, m'mawa ndi madzulo, pamasabata, ndi pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika za Yehova Mulungu wathu. Ndiwo machitidwe osatha mu Israele.