Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 29:25 - Buku Lopatulika

25 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi zopereka zake zachakudya ndi za chakumwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 29:25
13 Mawu Ofanana  

Ndipo anatenga malaya ake a Yosefe, napha tonde, naviika malaya m'mwazi wake:


tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo, pamodzi ndi nsembe yauchimo yotetezera, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira.


nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;


Ndi tsiku lachisanu ng'ombe zisanu ndi zinai, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, opanda chilema;


Chifukwa chake Yesu ananena kwa Ayuda aja adakhulupirira Iye, Ngati mukhala inu m'mau anga, muli ophunzira anga ndithu;


Ndipo m'mene anthu a m'sunagoge anabalalika, Ayuda ambiri ndi akupinduka opembedza anatsata Paulo ndi Barnabasi; amene, polankhula nao, anawaumiriza akhale m'chisomo cha Mulungu.


kwa iwo amene afunafuna ulemerero ndi ulemu ndi chisaonongeko, mwa kupirira pa ntchito zabwino, adzabwezera moyo wosatha;


Koma sitidawafumukire mowagonjera ngakhale ora limodzi; kuti choonadi cha Uthenga Wabwino chikhalebe ndi inu.


Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.


Koma inu, abale, musaleme pakuchita zabwino.


Koma ife si ndife a iwo akubwerera kulowa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.


Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.


pakuti takhala ife olandirana ndi Khristu, ngatitu tigwiritsa chiyambi cha kutama kwathu kuchigwira kufikira chitsiriziro;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa