Chomwecho pamene Ayuda onse okhala mu Mowabu ndi mwa ana a Amoni, ndi mu Edomu, ndi amene anali m'maiko monse, anamva kuti mfumu ya ku Babiloni inasiya otsala a Yuda, ndi kuti inamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani wolamulira wao;
Numeri 22:1 - Buku Lopatulika Ndipo ana a Israele anayenda ulendo, namanga mahema m'zigwa za Mowabu, tsidya la Yordani ku Yeriko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ana a Israele anayenda ulendo, namanga mahema m'zigwa za Mowabu, tsidya la Yordani ku Yeriko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aisraele adanyamuka ulendo nakamanga mahema ao m'zigwa za Amowabu patsidya pa Yordani ku Yeriko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aisraeli anayenda kupita ku zigwa za Mowabu nakamanga misasa yawo tsidya lina la Yorodani moyangʼanana ndi Yeriko. |
Chomwecho pamene Ayuda onse okhala mu Mowabu ndi mwa ana a Amoni, ndi mu Edomu, ndi amene anali m'maiko monse, anamva kuti mfumu ya ku Babiloni inasiya otsala a Yuda, ndi kuti inamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani wolamulira wao;
atachoka ku Bamoti ku chigwa chili m'dziko la Mowabu, ku mutu wa Pisiga, popenyana ndi chipululu.
Pamenepo Mose ndi Eleazara wansembe ananena nao m'zidikha za Mowabu pa Yordani kufupi ku Yeriko, ndi kuti,
Ndipo anadza nao andende, ndi zakunkhondo, ndi zofunkha, kwa Mose, ndi kwa Eleazara wansembe, ndi kwa khamu la ana a Israele, kuchigono, ku zidikha za Mowabu, zili ku Yordani pafupi pa Yeriko.
Pakuti sitidzalandira pamodzi nao tsidya la Yordani, ndi m'tsogolo mwake; popeza cholowa chathu tachilandira tsidya lino la Yordani kum'mawa.
mafuko awiriwa ndi hafu adalandira cholowa chao tsidya lija la Yordani ku Yeriko, kum'mawa, kotulukira dzuwa.
Awa ndi malamulo ndi maweruzo, amene Yehova analamulira ana a Israele ndi dzanja la Mose m'zidikha za Mowabu pa Yordani ku Yeriko.
Tsidya lija la Yordani, m'dziko la Mowabu, Mose anayamba kufotokozera chilamulo ichi, ndi kuti,
Ndipo muja tinalanda dziko m'manja mwa mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordani, kuyambira mtsinje wa Arinoni kufikira phiri la Heremoni;
Ndipo Mose anakwera kuchokera ku zidikha za Mowabu, kunka kuphiri la Nebo, pamwamba pa Pisiga, popenyana ndi Yeriko. Ndipo Yehova anamuonetsa dziko lonse la Giliyadi, kufikira ku Dani;
Ndipo ana a Israele analira Mose m'zidikha za Mowabu masiku makumi atatu; potero anatha masiku akulira maliro a Mose.
pamenepo madzi ochokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adama, ndiwo mzinda wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kunka ku nyanja ya chidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko.