Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 32:19 - Buku Lopatulika

19 Pakuti sitidzalandira pamodzi nao tsidya la Yordani, ndi m'tsogolo mwake; popeza cholowa chathu tachilandira tsidya lino la Yordani kum'mawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Pakuti sitidzalandira pamodzi nao tsidya la Yordani, ndi m'tsogolo mwake; popeza cholowa chathu tachilandira tsidya lino la Yordani kum'mawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Ife ndiye sitidzalandira nao choloŵa chathu patsidya pa Yordanipo kapena patsogolo pake, chifukwa choti talandira choloŵa chathu tsidya lino la Yordani, kuvuma kuno.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Sitidzalandira cholowa chilichonse pamodzi nawo ku tsidya lina la Yorodani, chifukwa cholowa chathu tachipezera ku tsidya lino la kummawa kwa Yorodani.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 32:19
11 Mawu Ofanana  

Ndipo anagwira Loti mwana wa Abramu amene anakhala mu Sodomu, ndi chuma chake, namuka.


Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya.


Cholowa chingalandiridwe msangamsanga poyamba pake; koma chitsiriziro chake sichidzadala.


mafuko awiriwa ndi hafu adalandira cholowa chao tsidya lija la Yordani ku Yeriko, kum'mawa, kotulukira dzuwa.


Pamodzi ndi iye Arubeni ndi Agadi analandira cholowa chao, chimene Mose adawapatsa tsidya ilo la Yordani kum'mawa, monga Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa