Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 21:35 - Buku Lopatulika

35 Ndipo anamkantha iye, ndi ana ake aamuna ndi anthu ake onse, kufikira sanatsale ndi mmodzi yense; nalanda dziko lake likhale laolao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 Ndipo anamkantha iye, ndi ana ake amuna ndi anthu ake onse, kufikira sanatsale ndi mmodzi yense; nalanda dziko lake likhale laolao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Choncho Aisraele adapha Ogi, ana ake aamuna ndi anthu ake onse, kotero kuti panalibe ndi mmodzi yemwe amene adatsalira, ndipo adalanda dziko lakelo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 Choncho Aisraeli anapha Ogi pamodzi ndi ana ake aamuna ndi gulu lake lonse la nkhondo. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala wamoyo, ndipo analanda dziko lakelo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 21:35
13 Mawu Ofanana  

dzikoli Yehova analikantha pamaso pa gulu la Israele, ndilo dziko la zoweta ndipo anyamata anu ali nazo zoweta.


Koma m'zonsezi, ife tilakatu, mwa Iye amene anatikonda.


Ndipo Ahori anakhala mu Seiri kale, koma ana a Esau analanda dziko lao, nawaononga pamaso pao, nakhala m'malo mwao; monga Israele anachitira dziko lakelake, limene Yehova anampatsa).


Ndipo Yehova adzawachitira monga anachitira Sihoni ndi Ogi, mafumu a Aamori, ndi dziko lao limene analiononga.


tsidya lija la Yordani, m'chigwa cha pandunji pa Betepeori, m'dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala mu Hesiboni, amene Mose ndi ana a Israele anamkantha, potuluka iwo mu Ejipito;


ndipo analanda dziko lake, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, mafumu awiri a Aamori, akukhala tsidya lija la Yordani lotuluka dzuwa;


ufumu wonse wa Ogi mu Basani, wa kuchita ufumu mu Asitaroti, ndi mu Ederei (yemweyo anatsala pa otsala a Arefaimu); pakuti Mose anakantha awa, nawainga.


Ndipo Yehova anati kwa ana a Israele, Kodi sindinakupulumutsani kwa Aejipito ndi kwa Aamori, ndi kwa ana a Amoni, ndi kwa Afilisti?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa