Ndipo Rubeni anabwera kudzenje, ndipo taonani, Yosefe mulibe m'dzenjemo: ndipo iye anang'amba nsalu yake.
Numeri 14:6 - Buku Lopatulika Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebe mwana wa Yefune, ndiwo a iwo aja adazonda dzikolo, anang'amba zovala zao; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebe mwana wa Yefune, ndiwo a iwo aja adazonda dzikolo, anang'amba zovala zao; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebe mwana wa Yefune, amene adaali m'gulu la anthu okazonda dziko lija, adang'amba zovala zao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yoswa mwana wa Nuni ndi Kalebe mwana wa Yefune, omwe anali amodzi mwa amene anakazonda nawo dziko, anangʼamba zovala zawo |
Ndipo Rubeni anabwera kudzenje, ndipo taonani, Yosefe mulibe m'dzenjemo: ndipo iye anang'amba nsalu yake.
Yakobo ndipo anang'amba malaya ake, na vala chiguduli m'chuuno mwake namlirira mwana wake masiku ambiri.
Ndipo Davide anati kwa Yowabu ndi kwa anthu onse okhala naye, Ng'ambani zovala zanu, ndi kudzimangira ziguduli m'chuuno, nimulire Abinere. Ndipo mfumu Davide anatsata chithatha.
Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba, ndi Sebina mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolembera mbiri, anadza kwa Hezekiya ndi zovala zao zong'ambika, namuuza mau a kazembeyo.
Pamenepo Yobu ananyamuka, nang'amba malaya ake, nameta mutu wake, nagwa pansi, nalambira,
Koma Kalebe anatontholetsa anthu pamaso pa Mose, nati, Tikwere ndithu ndi kulilandira lathulathu; popeza tikhozadi kuchita kumene.
koma mtumiki wanga Kalebe, popeza anali nao mzimu wina, nanditsata monsemo, ndidzamlowetsa iyeyu m'dziko muja analowamo; ndi mbeu zake zidzakhala nalo.
simudzalowa inu m'dzikolo, ndinakwezapo dzanja langa kukukhalitsani m'mwemo, koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo.
Koma Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebe mwana wa Yefune, anakhala ndi moyo mwa amuna aja adamukawo kukazonda dziko.
Pamenepo Mose ndi Aroni anagwa nkhope pansi pamaso pa msonkhano wonse wa khamu la ana a Israele.
nanena ndi khamu lonse la ana a Israele, nati, Dziko tapitamo kulizonda, ndilo dziko lokometsetsa ndithu.
Pomwepo mkulu wa ansembe anang'amba zovala zake, nati, Achitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina? Onani, tsopano mwamva mwanowo;
Pamenepo ana a Yuda anadza kwa Yoswa ku Giligala; ndi Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi ananena naye, Mudziwa chimene Yehova adanena kwa Mose munthu wa Mulungu za ine ndi za inu mu Kadesi-Baranea.
Ndipo Yoswa anang'amba zovala zake, nagwa nkhope yake pansi, ku likasa la Yehova, mpaka madzulo, iye ndi akuluakulu a Israele, nathira fumbi pamitu pao.
Ndipo kunali, pakumuona anang'amba zovala zake, nati, Tsoka ine, mwana wanga, wandiweramitsa kwakukulu, ndiwe wa iwo akundisaukitsa ine; pakuti ndamtsegulira Yehova pakamwa panga ine, ndipo sinditha kubwerera.