Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 14:30 - Buku Lopatulika

30 simudzalowa inu m'dzikolo, ndinakwezapo dzanja langa kukukhalitsani m'mwemo, koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 simudzalowa inu m'dzikolo, ndinakwezapo dzanja langa kukukhalitsani m'mwemo, koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaloŵe m'dziko limene ndidalumbira kuti mudzaloŵamo, kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene adzalowe mʼdziko lomwe ndinalumbira mokweza manja kuti likhale lanu, kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 14:30
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Abramu anati kwa mfumu ya Sodomu, Dzanja langa ndamtukulira Yehova, Mulungu Wamkulukulu, mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi


Chifukwa chake ndinalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga.


Ndipo ndidzakulowetsani m'dziko limene ndinakweza dzanja langa kunena za ilo, kuti ndilipereke kwa Abrahamu, kwa Isaki ndi kwa Yakobo; ndipo ndidzakupatsani ilo likhale lanulanu; Ine ndine Yehova.


Ndipo ndinawakwezeranso dzanja langa m'chipululu, kusawalowetsa m'dzikolo ndidawapatsa, moyenda mkaka ndi uchi, ndilo lokometsetsa mwa maiko onse;


ndipo ndidzasankhula mwa inu opanduka ndi ondilakwira, ndidzawatulutsa m'dziko logoneramo iwo; koma sadzalowa m'dziko la Israele; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


Wa fuko la Yuda, Kalebe mwana wa Yefune.


koma mtumiki wanga Kalebe, popeza anali nao mzimu wina, nanditsata monsemo, ndidzamlowetsa iyeyu m'dziko muja analowamo; ndi mbeu zake zidzakhala nalo.


Koma Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebe mwana wa Yefune, anakhala ndi moyo mwa amuna aja adamukawo kukazonda dziko.


Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m'chipululu. Ndipo sanatsalire mmodzi wa iwowa koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.


koma Kalebe mwana wa Yefune, Mkenizi, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo; popeza anatsata Yehova ndi mtima wonse.


nalumbira kutchula Iye amene ali ndi moyo kunthawi za nthawi, amene analenga m'mwamba ndi zinthu zili momwemo, ndi dziko lapansi ndi zinthu zili momwemo, ndi nyanja ndi zinthu zili momwemo kuti sipadzakhalanso nthawi:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa