Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 14:31 - Buku Lopatulika

31 Koma makanda anu, amene munanena za iwowa kuti adzakhala chakudya, amenewo ndidzawalowetsa, ndipo adzadziwa dzikolo mudalikana.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Koma makanda anu, amene munanena za iwowa kuti adzakhala chakudya, amenewo ndidzawalowetsa, ndipo adzadziwa dzikolo mudalikana.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Ana anu amene munkati adzagwidwa mu ukapolo, ndidzaŵaloŵetsa m'dzikomo, ndipo adzalidziŵa dziko limene inu mukunyozalo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Koma ana anu amene mukunena kuti adzatengedwa ngati katundu wolanda ku nkhondo, Ine ndidzawalowetsa kuti akasangalale mʼdziko limene munalikana.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 14:31
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anampatsa Esau mkate ndi mphodza zophika; ndipo iye anadya, namwa, nanyamuka, napita: chomwecho Esau ananyoza ukulu wake.


Nalowa anawo, nalandira dzikoli likhale laolao, ndipo munagonjetsa pamaso pao okhala m'dziko, ndiwo Akanani, ndi kuwapereka m'dzanja mwao, pamodzi ndi mafumu ao, ndi mitundu ya anthu ya m'dziko, kuti achite nao chifuniro chao.


Anapeputsanso dziko lofunika, osavomereza mau ake;


koma munapeputsa uphungu wanga wonse, ndi kukana kudzudzula kwanga.


anakana uphungu wanga, nanyoza kudzudzula kwanga konse;


Ndipo ndinati kwa ana ao m'chipululu, Musamayenda m'malemba a atate anu, musawasunga maweruzo ao, kapena kudzidetsa ndi mafano ao;


Ndipo Yehova atitengeranji kudza nafe kudziko kuno, kuti tigwe nalo lupanga? Akazi athu ndi makanda athu adzakhala chakudya chao; kodi sikuli bwino tibwerere ku Ejipito?


Hezironi, ndiye kholo la banja la Ahezironi; Karimi, ndiye kholo la banja la Akarimi.


Koma pakati pao panalibe mmodzi wa iwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Aroni wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'chipululu cha Sinai.


Koma iwo ananyalanyaza, nachoka, wina kumunda wake, wina kumalonda ake:


Taonani, opeputsa inu, zizwani, kanganukani; kuti ndigwiritsa ntchito Ine masiku anu, ntchito imene simudzaikhulupirira wina akakuuzani.


Ndipo ana anu amene mudanena, Adzakhala ogulidwa, ndi ana anu osadziwa chabwino kapena choipa ndi pano, iwo adzalowamo, ndidzawapatsa iwo ili, adzalilandira ndi iwo.


Koma ana ao aamuna amene anawautsa m'malo mwao, iwowa Yoswa anawadula; popeza anakhala osadulidwa, pakuti sanawadule panjira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa