Numeri 14:29 - Buku Lopatulika29 mitembo yanu idzagwa m'chipululu muno; ndi owerengedwa anu onse, monga mwa kuwerenga kwani konse, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, akudandaula pa Ine; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201429 mitembo yanu idzagwa m'chipululu muno; ndi owerengedwa anu onse, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, akudandaula pa Ine; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa29 Mitembo yanu idzakhala ili mbwee m'chipululu muno. Anthu onse, kuyambira a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo, amene adandiŵiringulira, Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero29 Mitembo yanu idzakhala ili ngundangunda mʼchipululu muno; mtembo wa munthu aliyense pakati panu amene ali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, amene anawerengedwa pa chiwerengero chija ndipo anangʼungʼudza motsutsana nane. Onani mutuwo |
Pakuti ana a Israele anayenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo otuluka mu Ejipito udatha, chifukwa cha kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi.