Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 14:28 - Buku Lopatulika

28 Nunene nao, Pali Ine ati Yehova, ndidzachitira inu ndithu monga mwanena m'makutu mwanga;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Nunene nao, Pali Ine ati Yehova, ndidzachitira inu ndithu monga mwanena m'makutu mwanga;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Uŵauze kuti, Chauta akunena kuti, ‘Zimene mwanena, Ine ndamva, ndipo ndi zimene ndidzakuchitani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Tsono awuze kuti, ‘Ndikulumbira pali Ine,’ akutero Yehova, ‘Ndidzakuchitirani zinthu zonse zimene ndamva inu mukunena:

Onani mutuwo Koperani




Numeri 14:28
18 Mawu Ofanana  

Aone yekha chionongeko chake m'maso mwake, namwe mkwiyo wa Wamphamvuyonse.


Potero anawasamulira dzanja lake, kuti awagwetse m'chipululu:


Chifukwa chake ndinalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga.


Pakuti Ine ndine Yehova, ndidzanena, ndi mau ndidzanenawo adzachitika, osazengerezekanso; pakuti m'masiku anu, nyumba yopanduka inu, ndidzanena mau ndi kuwachita, ati Yehova Mulungu.


Ndipo anthu anaipa, namadandaula m'makutu a Yehova; ndipo pamene Yehova anamva anapsa mtima; ndi moto wa Yehova unayaka pakati pao, nunyeketsa ku chilekezero cha chigono.


Ndipo ana onse a Israele anadandaulira Mose ndi Aroni; ndi khamu lonse linanena nao, Mwenzi tikadafa m'dziko la Ejipito; kapena mwenzi tikadafa m'chipululu muno!


koma ndithu, pali Ine, dziko lonse lapansi lidzadzazidwa ndi ulemerero wa Yehova;


sadzaona dzikoli ndidalumbirira makolo ao, ngakhale mmodzi wa iwo akundinyoza Ine, sadzaliona;


Ndipo Mose anauza ana a Israele mau onse awa; ndipo anthu anamva chisoni chambiri.


Anthu adakwerawo kutuluka mu Ejipito, kuyambira wa zaka makumi awiri ndi mphambu sadzaona dziko limene ndinalumbirira Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo; popeza sananditsate Ine ndi mtima wonse;


Ndipo Yehova anamva mau a kunena kwanu, nakwiya, nalumbira, ndi kuti,


Palibe mmodzi wa anthu awa a mbadwo uno woipa adzaona dziko lokomalo ndinalumbira kupatsa makolo anuli.


Ndipo masiku amene tinayenda kuchokera ku Kadesi-Baranea, kufikira tidaoloka mtsinje wa Zeredi, ndiwo zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu; kufikira utatha mbadwo wonse wa amuna ankhondo m'chigono, monga Yehova adawalumbirira.


Komanso dzanja la Yehova linatsutsana nao, kuwaononga m'chigono, kufikira adawatha.


Pakuti ndikweza dzanja langa kuloza kumwamba, ndipo nditi, Pali moyo wanga kosatha,


Koma anakwiya ndi ayani zaka makumi anai? Kodi si ndi awo adachimwawo, amene matupi ao adagwa m'chipululu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa