Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 14:24 - Buku Lopatulika

24 koma mtumiki wanga Kalebe, popeza anali nao mzimu wina, nanditsata monsemo, ndidzamlowetsa iyeyu m'dziko muja analowamo; ndi mbeu zake zidzakhala nalo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 koma mtumiki wanga Kalebe, popeza anali nao mzimu wina, nanditsata monsemo, ndidzamlowetsa iyeyu m'dziko muja analowamo; ndi mbeu zake zidzakhala nalo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Koma Kalebe mtumiki wanga, chifukwa ali ndi mtima wosiyana ndi ena, ndipo wanditsata ndi mtima wonse, ndidzamloŵetsa m'dziko limene adapitamolo, ndipo zidzukulu zake zidzalandira dzikolo kuti likhale lao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Koma mtumiki wanga Kalebe, pakuti ali ndi mtima wosiyana ndi ena ndiponso amanditsatira ndi mtima wonse, ndidzamulowetsa mʼdziko limene anapitamolo ndipo zidzukulu zake zidzalandira dzikolo ngati cholowa chawo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 14:24
17 Mawu Ofanana  

Yehova Mulungu wa Abrahamu, wa Isaki, ndi wa Israele makolo athu, musungitse ichi kosatha m'chilingaliro cha maganizo a mtima wa anthu anu, nimulunjikitse mitima yao kwanu,


Ndipo anthu anakondwera popeza anapereka mwaufulu; pakuti ndi mtima wangwiro anapereka mwaufulu kwa Yehova; mfumu Davide yemwe anakondwera ndi chimwemwe chachikulu.


Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosachita ndi mtima wangwiro.


Ndinaitana ndi mtima wanga wonse; mundiyankhe, Yehova; ndidzasunga malemba anu.


Mtima wanga ukhale wangwiro m'malemba anu; kuti ndisachite manyazi.


Mwananga, undipatse mtima wako, maso ako akondwere ndi njira zanga.


Koma Kalebe anatontholetsa anthu pamaso pa Mose, nati, Tikwere ndithu ndi kulilandira lathulathu; popeza tikhozadi kuchita kumene.


simudzalowa inu m'dzikolo, ndinakwezapo dzanja langa kukukhalitsani m'mwemo, koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo.


Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m'chipululu. Ndipo sanatsalire mmodzi wa iwowa koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.


ameneyo, m'mene anafika, naona chisomo cha Mulungu, anakondwa; ndipo anawadandaulira onse, kuti atsimikize mtima kukhalabe ndi Ambuye;


si monga mwa ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Khristu, akuchita chifuniro cha Mulungu chochokera kumtima;


Koma Kalebe mwana wa Yefune, iye adzaliona; ndidzampatsa iye dziko limene anapondapo, ndi ana ake; popeza analimbika ndi kutsata Yehova.


ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.


chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa