Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 14:14 - Buku Lopatulika

14 Pamene anamva atumwi Paulo ndi Barnabasi, anang'amba zofunda zao, natumphira m'khamu,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Pamene anamva atumwi Paulo ndi Barnabasi, anang'amba zofunda zao, natumphira m'khamu,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Koma pamene atumwi aja, Barnabasi ndi Paulo, adamva zimenezi, adang'amba zovala zao, nathamangira pakati pa anthuwo. Adalankhula mokweza mau kuti,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Koma Barnaba ndi Paulo atamva zimenezi, anangʼamba zovala zawo, nathamangira pakati pa gulu la anthuwo, akufuwula kuti,

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 14:14
11 Mawu Ofanana  

Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba, ndi Sebina mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolembera mbiri, anadza kwa Hezekiya ndi zovala zao zong'ambika, namuuza mau a kazembeyo.


Ndipo kunali atawerenga kalatayo mfumu ya Israele, anang'amba zovala zake, nati, Ngati ndine Mulungu, kupha ndi kubwezera moyo, kuti ameneyo atumiza kwa ine kumchiritsa munthu khate lake? Pakuti dziwani, nimupenye, kuti alikufuna chifukwa pa ine.


Ndipo sanaope, sanang'ambe nsalu zao, kapena mfumu, kapena atumiki ake aliyense amene anamva mau onsewa.


Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebe mwana wa Yefune, ndiwo a iwo aja adazonda dzikolo, anang'amba zovala zao;


Pomwepo mkulu wa ansembe anang'amba zovala zake, nati, Achitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina? Onani, tsopano mwamva mwanowo;


Ndipo mkulu wa ansembe anang'amba malaya ake, nanena, Tifuniranjinso mboni zina?


Ndipo khamu la mzindawo linagawikana; ena anali ndi Ayuda, koma ena anali ndi atumwi.


Kodi sindine mfulu? Kodi sindine mtumwi? Kodi sindinaone Yesu Ambuye wathu? Kodi simuli inu ntchito yanga mwa Ambuye?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa