Numeri 10:12 - Buku Lopatulika Ndipo ana a Israele anayenda monga mwa maulendo ao, kuchokera m'chipululu cha Sinai; ndi mtambo unakhala m'chipululu cha Parani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ana a Israele anayenda monga mwa maulendo ao, kuchokera m'chipululu cha Sinai; ndi mtambo unakhala m'chipululu cha Parani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Aisraele adanyamuka ulendo wao m'magulumagulu kuchokera ku chipululu cha Sinai. Mtambowo udakaima m'chipululu cha Parani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Aisraeli ananyamuka kuchoka mʼchipululu cha Sinai ndipo anayenda malo osiyanasiyana mpaka pamene mtambo unayima mʼchipululu cha Parani. |
Ndipo anakhala m'chipululu cha Parani; ndipo amake anamtengera iye mkazi wa ku dziko la Ejipito.
Ndipo anachoka ku Midiyani nafika ku Parani, natenga anthu a ku Parani pamodzi nao, nafika ku Ejipito kwa Farao mfumu ya Aejipito, ameneyo anampatsa nyumba, namnenera zakudya, nampatsako dziko.
Mulungu anafuma ku Temani, ndi Woyerayo kuphiri la Parani. Ulemerero wake unaphimba miyamba, ndi dziko lapansi linadzala ndi kumlemekeza.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, m'chihema chokomanako, tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, chaka chachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito, ndi kuti,
Ndipo anayenda kuchokera kuphiri la Yehova ulendo wa masiku atatu; ndipo likasa la chipangano cha Yehova, linawatsogolera ulendo wa masiku atatu kuwafunira popumulira.
Ndipo atatero anthuwo ananka ulendo wao kuchokera ku Hazeroti, namanga mahema ao m'chipululu cha Parani.
Ndipo anamuka, nadza kwa Mose, ndi Aroni, ndi khamu lonse la ana a Israele, ku chipululu cha Parani ku Kadesi; ndipo anabwezera mau iwowa, ndi khamu lonse, nawaonetsa zipatso za dzikoli.
Ndipo Mose anawatumiza kuchokera ku chipululu cha Parani monga mwa mau a Yehova; amuna onsewa ndiwo akulu a ana a Israele.
Ndipo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo anamanga mahema ao pa mbendera zao, momwemonso anayenda paulendo, yense monga mwa mabanja ake, monga mwa nyumba za makolo ake.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, mwezi woyamba wa chaka chachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito, ndi kuti,
Ndipo pokwera mtambo kuchokera kuchihema, utatero ana a Israele amayenda ulendo wao; ndipo pamalo pokhala mtambo, pamenepo ana a Israele amamanga mahema ao.
Ndipo anachita Paska mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo m'chipululu cha Sinai; monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo ana a Israele anachita.
Awa ndi mau amene Mose ananena kwa Israele wonse, tsidya la Yordani m'chipululu, m'chidikha cha pandunji pa Sufu, pakati pa Parani, ndi Tofele, ndi Labani, ndi Hazeroti, ndi Dizahabu.
Pamenepo tinayenda ulendo kuchokera ku Horebu, ndi kubzola m'chipululu chachikulu ndi choopsa chija chonse munachionachi, panjira ya ku mapiri a Aamori, monga Yehova Mulungu wathu anatiuza; ndipo tinadza ku Kadesi-Baranea.
bwererani, yendani ulendo wanu ndi kumuka ku mapiri a Aamori, ndi koyandikizana nao, kuchidikha, kumapiri, ndi kunsi ndi kumwera, ndi kumphepete kwa nyanja, dziko la Akanani, ndi Lebanoni, kufikira mtsinje waukulu wa Yufurate.
Ndipo anati, Yehova anafuma ku Sinai, nawatulukira ku Seiri; anaoneka wowala paphiri la Parani, anafumira kwa opatulika zikwizikwi; ku dzanja lamanja lake kudawakhalira lamulo lamoto.
Ndipo Samuele anamwalira; ndi Aisraele onse anaunjikana pamodzi nalira maliro ake, namuika m'nyumba yake ku Rama. Davide ananyamuka, natsikira ku chipululu cha Parani.