Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 25:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo Samuele anamwalira; ndi Aisraele onse anaunjikana pamodzi nalira maliro ake, namuika m'nyumba yake ku Rama. Davide ananyamuka, natsikira ku chipululu cha Parani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Samuele anamwalira; ndi Aisraele onse anaunjikana pamodzi nalira maliro ake, namuika m'nyumba yake ku Rama. Davide ananyamuka, natsikira ku chipululu cha Parani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Samuele adamwalira. Ndipo Aisraele onse adasonkhana kudzalira maliro ake, namuika kumudzi kwao ku Lama. Masiku amenewo Davide adanyamuka, napita ku chipululu cha Parani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Samueli anamwalira, ndipo Aisraeli onse anasonkhana kudzalira maliro ake ndipo anamuyika mʼmanda ku mudzi kwawo ku Rama. Ndipo Davide anapita ku chipululu cha Parani.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 25:1
20 Mawu Ofanana  

ndi Ahori paphiri lao Seiri kufikira ku Eliparani, kumene kuli m'mbali mwa chipululu.


Ndipo anakhala m'chipululu cha Parani; ndipo amake anamtengera iye mkazi wa ku dziko la Ejipito.


Ndipo Sara anafa mu Kiriyati-Ariba (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani; ndipo Abrahamu anadza ku maliro a Sara, kuti amlire.


Ndipo pamene anthu okhala m'dzikomo, Akanani, anaona maliro a m'dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro aakulu a Aejipito: chifukwa chake dzina la pamenepo linatchedwa Abele-Mizraimu, pali tsidya lija la Yordani.


Pomwepo Benaya mwana wa Yehoyada anakwera namkantha iye, namupha; ndipo anaikidwa m'nyumba yakeyake kuchipululu.


Nagona Manase ndi makolo ake, naikidwa m'munda wa nyumba yake, m'munda wa Uza, nakhala mfumu m'malo mwake Amoni mwana wake.


Momwemo Manase anagona ndi makolo ake, namuika m'nyumba mwakemwake; ndi Amoni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Tsoka ine, kuti ndili mlendo mu Meseki, kuti ndigonera m'mahema a Kedara!


Mafumu onse a amitundu, onsewo agona mu ulemerero yense kunyumba kwake.


Makolo anu, ali kuti iwowo? Ndi aneneri, akhala ndi moyo kosatha kodi?


Ndipo ana a Israele anayenda monga mwa maulendo ao, kuchokera m'chipululu cha Sinai; ndi mtambo unakhala m'chipululu cha Parani.


Ndipo atatero anthuwo ananka ulendo wao kuchokera ku Hazeroti, namanga mahema ao m'chipululu cha Parani.


Ndipo anamuka, nadza kwa Mose, ndi Aroni, ndi khamu lonse la ana a Israele, ku chipululu cha Parani ku Kadesi; ndipo anabwezera mau iwowa, ndi khamu lonse, nawaonetsa zipatso za dzikoli.


Ndipo Mose anawatumiza kuchokera ku chipululu cha Parani monga mwa mau a Yehova; amuna onsewa ndiwo akulu a ana a Israele.


Pamene khamu lonse linaona kuti Aroni adamwalira, anamlira Aroni masiku makumi atatu, ndiyo mbumba yonse ya Israele.


Ndipo anamuika Stefano anthu opembedza, namlira maliro aakulu.


Ndipo ana a Israele analira Mose m'zidikha za Mowabu masiku makumi atatu; potero anatha masiku akulira maliro a Mose.


Ndipo iwo anauka mamawa, nalambira pamaso pa Yehova, nabwerera, nafikanso kwao ku Rama; ndipo Elikana anadziwa mkazi wake Hana, Yehova namkumbukira iye.


M'menemo Samuele ndipo atafa, ndipo Aisraele onse atalira maliro ake, namuika mu Rama, m'mzinda mwao. Ndipo Saulo anachotsa m'dzikomo obwebweta onse, ndi aula onse.


Ndipo anabwera ku Rama, pakuti nyumba yake inali kumeneko; ndipo pamenepo anaweruza Israele; namangapo guwa la nsembe la Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa