Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 9:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo pokwera mtambo kuchokera kuchihema, utatero ana a Israele amayenda ulendo wao; ndipo pamalo pokhala mtambo, pamenepo ana a Israele amamanga mahema ao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo pokwera mtambo kuchokera kuchihema, utatero ana a Israele amayenda ulendo wao; ndipo pamalo pokhala mtambo, pamenepo ana a Israele amamanga mahema ao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Mtambowo ukangokwera kuchoka pachihemapo, Aisraele ankanyamuka ulendo; ndipo pamene mtambowo unkakaima, Aisraele ankamanga mahema ao pamalo pamenepo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Nthawi ina iliyonse mtambo ukachoka pamwamba pa chihema, Aisraeli ankasamukanso, ndipo paliponse pamene mtambo wayima, Aisraeli ankamangapo misasa.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 9:17
12 Mawu Ofanana  

Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.


Mudzanditsogolera ndi uphungu wanu, ndipo mutatero, mudzandilandira mu ulemerero.


Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka m'chipululu cha Sini, M'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona mu Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu.


Iwo sadzakhala ndi njala, pena ludzu; ngakhale thukuta, pena dzuwa silidzawatentha; pakuti Iye amene wawachitira chifundo, adzawatsogolera, ngakhale pa akasupe a madzi adzawatsogolera.


Ngakhale masiku awiri, kapena mwezi, kapena masiku ambiri, pokhalitsa mtambo pamwamba pa chihema ndi kukhalapo, ana a Israele anakhala m'chigono, osayenda ulendo; koma pakukwera uwu, anayenda ulendo.


Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulumutsidwa, nadzalowa, nadzatuluka, nadzapeza busa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa