Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 9:18 - Buku Lopatulika

18 Pakuwauza Yehova ana a Israele amayenda ulendo, powauza Yehova amamanga mahema ao; masiku onse mtambo ukakhala pamwamba pa chihema amakhala m'chigono.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Pakuwauza Yehova ana a Israele amayenda ulendo, powauza Yehova amamanga mahema ao; masiku onse mtambo ukakhala pamwamba pa Kachisi amakhala m'chigono.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Aisraele ankanyamuka ulendo wao Chauta akaŵalamula, ndipo ankamanga mahema ao Chauta akaŵalamula. Nthaŵi yonse pamene mtambowo unali pa chihemacho, iwo ankakhalabe m'mahema.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Aisraeli ankasamuka pamalopo Yehova akawalamula, ndipo ankamanganso misasa Iyeyo akawalamula. Nthawi yonse imene mtambowo wayima pa chihema, ankakhalabe mʼmisasa yawo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 9:18
7 Mawu Ofanana  

Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka m'chipululu cha Sini, M'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona mu Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu.


Potero anayamba ulendo wao monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose.


Kudatero kosalekeza; mtambo umachiphimba, ndi moto umaoneka usiku.


Ndipo pakukhalitsa mtambo masiku ambiri pamwamba pa chihema, pamenepo ana a Israele anasunga udikiro wa Yehova osayenda ulendo.


Ndipo pokhala mtambo pamwamba pa chihema masiku pang'ono; pamenepo anakhala m'chigono monga awauza Yehova, nayendanso ulendo monga anauza Yehova.


Pakuti sindifuna, kuti mukhale osadziwa, abale, kuti makolo athu onse anali pansi pa mtambo, naoloka nyanja onse;


Ndipo chikondi ndi ichi, kuti tiyende monga mwa malamulo ake. Ili ndi lamulolo, monga mudalimva kuyambira pachiyambi, kuti mukayende momwemo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa