Mika 5:1 - Buku Lopatulika Uzisonkhana tsopano magulumagulu, mwana wamkazi wa magulu iwe; watimangira misasa, adzapanda woweruza wa Israele ndi ndodo patsaya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Uzisonkhana tsopano magulumagulu, mwana wamkazi wa magulu iwe; watimangira misasa, adzapanda woweruza wa Israele ndi ndodo patsaya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsopano konzekani m'magulu ankhondo, inu a ku Yerusalemu. Atizinga ndi zithando zankhondo, akuthira nkhondo likulu la Israele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwe mzinda wa anthu ankhondo, sonkhanitsa anthu ako ankhondo, pakuti anthu atizungulira kuti alimbane nafe. Adzakantha ndi ndodo pa chibwano cha wolamulira wa Israeli. |
Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.
Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenana anasendera, napanda Mikaya patsaya, nati, Mzimu wa Yehova wandichokera bwanji, kulankhula ndi iwe?
Ndipo Yehova anamtumizira magulu a Ababiloni, ndi magulu a Aaramu, ndi magulu a Amowabu, ndi magulu a ana a Amoni, nawatumiza pa Yuda kuliononga, monga mwa mau a Yehova adawanena ndi dzanja la atumiki ake aneneriwo.
Iwo anandiyasamira pakamwa pao; anandiomba pama ndi kunditonza; asonkhana pamodzi kunditsutsa.
Ine ndidzamtumiza kumenyana ndi mtundu wosalemekeza, ndi pa anthu a mkwiyo wanga ndidzamlangiza, kuti afunkhe, agwire zolanda, awapondereze pansi, monga dothi la pamakwalala.
Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.
Chitani phokoso, anthu inu, koma mudzathyokathyoka; tcherani khutu, inu nonse a maiko akutali; kwindani nokha, koma mudzathyokathyoka; kwindani nokha, koma mudzathyokathyoka.
Pakuti zida zonse za mwamuna wovala zida za nkhondo m'phokosomo, ndi zovala zomvimvinika m'mwazi, zidzakhala zonyeka ngati nkhuni.
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.
Mkango wakwera kutuluka m'nkhalango mwake, ndipo waononga amitundu ali panjira, watuluka m'mbuto mwake kuti achititse dziko lako bwinja, kuti mizinda yako ipasuke mulibenso wokhalamo.
Udzakhala ngati nkhuni ya pamoto, mwazi wako udzakhala pakati padziko, sudzakumbukikanso; pakuti Ine ndine Yehova ndachinena.
Wobadwa ndi munthu iwe, Udzilembere dzina la tsiku lomwe lino, mfumu ya ku Babiloni wayandikira Yerusalemu tsiku lomwe lino.
Dziwa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri makwalala ndi tchemba zidzamangidwanso, koma mu nthawi za mavuto.
Mulalikire ichi mwa amitundu, mukonzeretu nkhondo; utsani amuna amphamvu; amuna onse a nkhondo ayandikire nakwere.
Pakuti taonani, ndiukitsa Ababiloni, mtundu uja wowawa ndi waliwiro, wopitira pa chitando cha dziko lapansi, kulowa m'malo mosati mwao, mukhale mwaomwao.
Ndinamva, ndi m'mimba mwanga munabwadamuka, milomo yanga inanthunthumira pamau, m'mafupa mwanga mudalowa chivundi, ndipo ndinanjenjemera m'malo mwanga; kuti ndipumule tsiku lamsauko, pamene akwerera anthu kuti ayambane nao ndi makamu.
koma ndinena kwa inu, Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe pa tsaya lako lamanja, umtembenuzire linanso.
Koma m'mene Iye adanena izi, mmodzi wa anyamata akuimirirako anapanda Yesu khofu, ndi kuti, Kodi uyankha mkulu wa ansembe chomwecho?
Pakuti mulola ngati wina akuyesani inu akapolo, ngati wina alikwira inu, ngati wina alanda zanu, ngati wina adzikuza, ngati wina akupandani pankhope.
Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wochokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamve malankhulidwe ao;
Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako; ndi pansipo pali manja osatha. Ndipo aingitsa mdani pamaso pako, nati, Ononga.
Ndipo panali mnyamata wa ku Betelehemu ku Yuda, wa banja la Yuda, ndiye Mlevi, nagonera iye komweko.