Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 4:7 - Buku Lopatulika

7 Mkango wakwera kutuluka m'nkhalango mwake, ndipo waononga amitundu ali panjira, watuluka m'mbuto mwake kuti achititse dziko lako bwinja, kuti mizinda yako ipasuke mulibenso wokhalamo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Mkango wakwera kutuluka m'nkhalango mwake, ndipo woononga amitundu ali panjira, watuluka m'mbuto mwake kuti achititse dziko lako bwinja, kuti midzi yako ipasuke mulibenso wokhalamo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Monga momwe mkango umatulukira m'ngaka yake, momwemonso woononga maiko wanyamuka. Watuluka m'malo mwake kuti asakaze dziko lanu. Mizinda yanu idzakhala mabwinja popanda okhalamo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Monga mkango umatulukira mʼngaka yake momwemonso wowononga mayiko wanyamuka ndi kutuluka ku mbuto yake. Watero kuti awononge dziko lanu. Mizinda yanu idzakhala mabwinja popanda wokhalamo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 4:7
33 Mawu Ofanana  

Masiku ake Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anakwerako, Yehoyakimu nagwira mwendo wake zaka zitatu; pamenepo anatembenuka nampandukira.


Ndipo kunali chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wake, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, iye ndi khamu lake lonse anadzera Yerusalemu, naumangira misasa, naumangira timalinga mouzinga.


Dziko lanu lili bwinja; mizinda yanu yatenthedwa ndi moto; dziko lanu alendo alimkudya pamaso panu; ndipo lili labwinja monga lagubuduzidwa ndi alendo.


M'makutu anga, ati Yehova wa makamu, Zoonadi nyumba zambiri zidzakhala bwinja, ngakhale zazikulu ndi zokoma zopanda wokhalamo.


Pompo ndinati ine, Ambuye mpaka liti? Ndipo anayankha, Mpaka mizinda ikhala bwinja, yopanda wokhalamo, ndi nyumba zopanda munthu, ndi dziko likhala bwinja ndithu,


Ana a mikango anambangulira iye, nakweza mau; anapasula dziko lake, mizinda yake yatenthedwa, mulibenso wokhalamo.


Pakuti Yehova atero za nyumba ya mfumu ya Yuda: Ndikuyesa iwe Giliyadi, ndi mutu wa Lebanoni; koma ndidzakuyesa iwe chipululu, ndi mizinda yosakhalamo anthu.


Ndipo ndidzakupangiratu iwe opasula, yense ndi zida zake; ndipo adzadula mikungudza yako yosankhika nadzaiponya m'moto.


Wasiya ngaka yake, monga mkango; pakuti dziko lao lasanduka chizizwitso chifukwa cha ukali wa lupanga losautsa, ndi chifukwa cha mkwiyo wake waukali.


taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.


Bwanji mwanenera m'dzina la Yehova, kuti, Nyumba iyi idzafanana ndi Silo, mzinda uwu udzakhala bwinja lopanda wokhalamo? Ndipo anthu onse anamsonkhanira Yeremiya m'nyumba ya Yehova.


Ndipo padzakhala, kuti mtundu ndi ufumu umene sudzamtumikira Nebukadinezara yemweyo mfumu ya ku Babiloni, mtundu umenewo Ine ndidzalanga, ati Yehova, ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, mpaka nditatha onse ndi dzanja lake.


Atero Yehova: M'malo muno, m'mene muti, Ndi bwinja, mopanda munthu, mopanda nyama, m'mizinda ya Yuda, m'makwalala a Yerusalemu, amene ali bwinja, opanda munthu, opanda wokhalamo, opanda nyama,


Taonani, ndidzauza, ati Yehova, ndidzabwezera iwo kumzinda uno; ndipo adzamenyana nao, nadzaulanda, nadzautentha ndi moto; ndipo ndidzayesa mizinda ya Yuda mabwinja, palibenso wokhalamo.


Mzinda wonse uthawa m'phokoso la apakavalo ndi amauta; adzalowa m'nkhalango, adzakwera pamiyala; mizinda yonse idzasiyidwa, ndipo simudzakhala munthu m'menemo.


Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Mwaona choipa chonse chimene ndatengera pa Yerusalemu, ndi pa mizinda yonse ya Yuda; ndipo, taonani, lero lomwe ili bwinja, palibe munthu wokhalamo;


Pali Ine, ati Mfumu, dzina lake ndi Yehova wa makamu, ndithu monga Tabori mwa mapiri, monga Karimele pambali pa nyanja, momwemo adzafika.


Taona, wina adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wochokera ku Yordani wosefuka; koma dzidzidzi ndidzamthamangitsa amchokere; ndipo aliyense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wake, pakuti wakunga Ine ndani? Adzandiikira nthawi ndani? Ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?


Chifukwa chake mkango wotuluka m'nkhalango udzawapha, ndi mmbulu wa madzulo udzawafunkha, nyalugwe adzakhalira m'mizinda mwao, onse amene atulukamo adzamwetulidwa; pakuti zolakwa zili zambiri, ndi mabwerero ao achuluka.


Israele ndiye nkhosa yolowerera, mikango yampirikitsa, poyamba inamudya mfumu ya Asiriya; ndipo pomaliza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wathyola mafupa ake.


Taonani, mtundu uja adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wochokera ku Yordani wosefuka; koma dzidzidzi ndidzauthamangitsa umchokere, ndipo aliyense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wake; pakuti wakunga Ine ndani? Adzandiikira nthawi ndani? Ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?


Kumina kwa akavalo ake kunamveka ku Dani; dziko lonse linanthunthumira pa kulira kwa akavalo akewo olimba; chifukwa afika, nadya dziko ndi zonse za momwemo; mzinda ndi amene akhalamo.


Ndipo ndidzayesa Yerusalemu miyulu, mbuto ya ankhandwe; ndipo ndidzayesa mizinda ya Yuda bwinja, lopanda wokhalamo.


Ndi mizinda yokhalamo anthu idzapasuka, ndi dziko lidzakhala labwinja; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


Ndipo ndidzakutsanulira mkwiyo wanga, ndidzakuuzira ndi moto wa kuzaza kwanga, ndidzakuperekanso m'manja mwa anthu ankharwe odziwa kuononga.


Wobadwa ndi munthu iwe, takwezera Farao mfumu ya Aejipito nyimbo yamaliro; uziti naye, Unafanana nao msona wa mkango wa amitundu, unanga ng'ona ya m'nyanja, unabuka m'mitsinje mwako, nuvundulira madzi ndi mapazi ako, ndi kudetsa mitsinje yao.


ndipo chifukwa cha ukulu adampatsawo anthu onse, mitundu yonse ya anthu, amanenedwe onse, ananjenjemera, naopa pamaso pake; amene anafuna kuwapha anawapha; amene anafuna kuwasunga anawasunga amoyo; amene anafuna kuwakweza anawakweza; amene anafuna kuwatsitsa anawatsitsa.


Choyamba chinanga mkango, chinali nao mapiko a chiombankhanga, ndinapenyera mpaka nthenga zake zinathothoka, ndipo chinakwezeka kudziko, ndi kuimitsidwa ndi mapazi awiri ngati munthu, ndipo chinapatsidwa mtima wa munthu.


Ndipo ndidzasandutsa mizinda yanu bwinja, ndi kupasula malo anu opatulika, wosanunkhiza Ine za fungo lanu lokoma.


Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi mizinda yanu idzakhala bwinja.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa