Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 4:8 - Buku Lopatulika

8 Pamenepo, valani chiguduli, lirani ndi kubuula; pakuti mkwiyo wa kuopsa wa Yehova sunabwerere pa ife.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Pamenepo, valani chiguduli, lirani ndi kubuula; pakuti mkwiyo wa kuopsa wa Yehova sunabwerera pa ife.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Motero valani ziguduli, mudandaule ndi kulira kwambiri. Pakuti mkwiyo woopsa wa Chauta sudatichoke.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Choncho valani ziguduli, lirani ndi kubuwula, pakuti mkwiyo waukulu wa Yehova sunatichokere.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 4:8
22 Mawu Ofanana  

Anawatumizira mkwiyo wake wotentha, kuzaza, ndi kupsa mtima, ndi nsautso, ndizo gulu la amithenga ochita zoipa.


Adzangoweramira pansi pa andende, ndipo adzagwa pansi pa ophedwa. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Kuwani inu; pakuti tsiku la Yehova lili pafupi; lidzafika monga chionongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.


Ndipo tsiku limenelo Ambuye, Yehova wa makamu, anaitana kulira, ndi kugwa misozi, ndi kumeta, ndi kuvala chiguduli m'chuuno;


Nthunthumirani, inu akazi, amene mulinkukhala phee; vutidwani, inu osasamalira, vulani mukhale maliseche, nimumange chiguduli m'chuuno mwanu.


Chifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayaka pa anthu ake, ndipo Iye watambasulira iwo dzanja lake, nawakantha, ndipo zitunda zinanthunthumira, ndi mitembo yao inali ngati zinyatsi pakati pa makwalala. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Aramu patsogolo ndi Afilisti pambuyo; ndipo iwo adzadya Israele ndi kukamwa koyasama. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Chifukwa chake Ambuye sadzakondwera ndi anyamata ao, ngakhale kuwachitira chifundo amasiye ao ana ndi akazi; popeza yense ali wodetsa ndi wochimwa, m'kamwa monse mulankhula zopusa. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Manase adzadya Efuremu; ndi Efuremu adzadya Manase, ndipo iwo pamodzi adzadyana ndi Yuda. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Kuwani, inu abusa, lirani, gubudukani, inu akulu a zoweta; pakuti masiku a kuphedwa kwanu akwanira ndithu, ndipo ndidzakuphwanyani inu, ndipo mudzagwa ngati chotengera chofunika.


Mkwiyo waukali wa Yehova sudzabwerera, mpaka wachita, mpaka watha zomwe afuna kuchita m'mtima mwake: masiku akumaliza mudzachizindikira.


Mowabu wachitidwa manyazi, pakuti wathyoka; kuwa nulire, nunene mu Arinoni, kuti Mowabu wapasuka.


Iwe mwana wamkazi wa anthu anga, udziveke ndi chiguduli, ndi kumvimvinika m'phulusa; ulire maliro ngati a mwana wamwamuna wa yekha, kulira kowawa koposa; pakuti wakufunkha adzatifikira ife motidzidzimutsa.


Kodi muyesa chimenechi chabe, nonsenu opita panjira? Penyani nimuone, kodi chilipo chisoni china ngati changachi amandimvetsa ine, chimene Yehova wandisautsa nacho tsiku la mkwiyo wake waukali?


Fuula ndi kulira, wobadwa ndi munthu iwe, pakuti likhalira pa anthu anga, likhalira pa akalonga onse a Israele, laperekedwa kulupanga pamodzi ndi anthu anga; chifukwa chake panda pantchafu pako.


Wobadwa ndi munthu iwe, nenera, uziti, Atero Ambuye Yehova, Liritsani, Ha, tsikulo!


Mudzimangire chiguduli m'chuuno mwanu, nimulire, ansembe inu; bumani otumikira kuguwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m'chiguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu.


Ndipo ndidzasanduliza zikondwerero zanu zikhale maliro, ndi nyimbo zanu zikhale za maliro, ndi kufikitsa ziguduli m'chuuno monse, ndi mpala pamutu uliwonse; nadzakhala ngati maliro a mwana mmodzi yekha, ndi chitsiriziro chake ngati tsiku lowawa.


Udziyeseze wadazi, udzimete wekha chifukwa cha ana ako okondwera nao; kuza dazi lako ngati la muimba; pakuti anakuchokera, nalowa ndende.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Gwira akulu onse a anthu nuwapachikire Yehova, pali dzuwa poyera, kuti mkwiyo waukali wa Yehova uchoke kwa Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa