Yeremiya 4:6 - Buku Lopatulika6 Kwezani mbendera kuyang'ana ku Ziyoni; thawani kuti mupulumuke, musakhale; pakuti ndidza ndi choipa chochokera kumpoto ndi kuononga kwakukulu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Kwezani mbendera kuyang'ana ku Ziyoni; thawani kuti mupulumuke, musakhale; pakuti ndidza ndi choipa chochokera kumpoto ndi kuononga kwakukulu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Kwezani mbendera ku Ziyoni. Musachedwe, thaŵani kuti mupulumuke. Chauta akubweretsa chilango kuchokera kumpoto, kudzakhala chiwonongeko chachikulu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Kwezani mbendera kuyangʼana ku Ziyoni! Musachedwe, thawani kuti mupulumuke! Pakuti Ine ndikubweretsa chilango kuchokera kumpoto, kudzakhala chiwonongeko choopsa.” Onani mutuwo |
Ndipo pambuyo pake, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ake, ndi anthu, ngakhale a m'mzinda uwu amene asiyidwa ndi mliri, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osachita chisoni, osachita chifundo.
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.