Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 4:5 - Buku Lopatulika

5 Nenani mu Yuda, lalikirani mu Yerusalemu, ndi kuti, Ombani lipenga m'dzikomo; fuulani, ndi kuti, Sonkhanani pamodzi, tilowe m'mizinda ya malinga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Nenani m'Yuda, lalikirani m'Yerusalemu, ndi kuti, Ombani lipenga m'dzikomo; fuulani, ndi kuti, Sonkhanani pamodzi, tilowe m'midzi ya malinga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Lalika ku Yuda, lengeza ku Yerusalemu kuti, “Lizani lipenga m'dziko lonse, ndi kufuula kuti, ‘Sonkhanani, tiyeni tipite ku mizinda ku Ziyoni.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 “Lengeza ku Yuda ndi kulalikira mu Yerusalemu kuti, ‘Lizani lipenga mʼdziko lonse!’ Ndipo fuwulani kuti, ‘Sonkhanani! Tiyeni tithawire ku mizinda yotetezedwa!’

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 4:5
16 Mawu Ofanana  

Nthawi zonse umapita, udzakutengani; chifukwa m'mawa ndi m'mawa udzapita, usana ndi usiku; ndipo kudzakhala kuopsa kokha, kumva mbiri yake.


Imvani mau a pangano ili, nenani kwa anthu a Yuda, ndi anthu a Yerusalemu;


Koma panali, pamene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anadza m'dzikomu, ife tinati, Tiyeni tinke ku Yerusalemu chifukwa tiopa nkhondo ya Ababiloni, ndi nkhondo ya Aramu; ndipo tikhala mu Yerusalemu.


Nenani ichi m'nyumba ya Yakobo, lalikirani mu Yuda, kuti,


Ananu a Benjamini, pulumukani pothawa pakati pa Yerusalemu, ombani lipenga mu Tekowa, kwezani chizindikiro mu Betehakeremu; pakuti chaoneka choipa chotuluka m'mpoto ndi kuononga kwakukulu.


Tikhaliranji ife? Tasonkhanani, tilowe m'mizinda yamalinga, tikhale chete m'menemo; pakuti Yehova Mulungu wathu watikhalitsa ife chete, natipatsa ife madzi a ndulu timwe, pakuti tamchimwira Yehova.


Wanzeru ndani, kuti adziwe ichi? Ndani iye amene kamwa la Yehova lanena naye, kuti achilalikire? Chifukwa chake dziko litha ndi kupserera monga chipululu, kuti anthu asapitemo?


Aomba lipenga, nakonzeratu zonse, koma palibe womuka kunkhondo; pakuti mkwiyo wanga ukhalira unyinji wake wonse.


Lipenga kukamwa kwako. Akudza ngati chiombankhanga, kulimbana ndi nyumba ya Yehova; chifukwa analakwira chipangano changa, napikisana nacho chilamulo changa.


Muombe lipenga mu Ziyoni, nimufuulitse m'phiri langa lopatulika; onse okhala m'dziko anjenjemere; pakuti tsiku la Yehova lilinkudza, pakuti liyandikira;


Kodi adzaomba lipenga m'mzinda osanjenjemera anthu? Kodi choipa chidzagwera mzinda osachichita Yehova?


Mkango ukabangula, ndani amene saopa? Ambuye Yehova wanena, ndani amene sanenera?


Dzipangire malipenga awiri asiliva; uwasule mapangidwe ake; uchite nao poitana khamu, ndi poyendetsa a m'zigono.


Akaliza, khamu lonse lisonkhane kuli iwe ku khomo la chihema chokomanako.


Ndipo kunali, Yoswa ndi ana a Israele atatha kuwakantha, makanthidwe aakulukulu mpaka atatha psiti, ndipo otsala a iwo atalowa m'mizinda ya malinga,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa