2 Mafumu 24:2 - Buku Lopatulika2 Ndipo Yehova anamtumizira magulu a Ababiloni, ndi magulu a Aaramu, ndi magulu a Amowabu, ndi magulu a ana a Amoni, nawatumiza pa Yuda kuliononga, monga mwa mau a Yehova adawanena ndi dzanja la atumiki ake aneneriwo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Ndipo Yehova anamtumizira magulu a Ababiloni, ndi magulu a Aaramu, ndi magulu a Amowabu, ndi magulu a ana a Amoni, nawatumiza pa Yuda kuliononga, monga mwa mau a Yehova adawanena ndi dzanja la atumiki ake aneneriwo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Tsono Chauta adatumiza magulu ankhondo a Ababiloni, a Asiriya, a Amowabu, ndi a Aamoni kuti akathire nkhondo Yuda, mpaka kuwononga dzikolo, monga momwe Chauta adaanenera kudzera mwa atumiki ake aneneri. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Yehova anatumiza magulu a Ababuloni, Aaramu, Amowabu ndi Aamoni, kudzathira nkhondo Yuda. Iye anawatumiza kudzawononga Yuda molingana ndi mawu amene Yehova ananeneratu kudzera mwa aneneri ake. Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.