Mateyu 9:12 - Buku Lopatulika Ndipo m'mene Yesu anamva anati, Olimba safuna sing'anga ai, koma odwala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'mene Yesu anamva anati, Olimba safuna sing'anga ai, koma odwala. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu atamva zimenezo, adaŵayankha kuti, “Anthu amene ali bwino sasoŵa sing'anga ai, koma amene akudwala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu atamva, anati, “Munthu wamoyo safuna singʼanga ayi, koma wodwala. |
Ndinati ine, Mundichitire chifundo, Yehova; Chiritsani mtima wanga; pakuti ndachimwira Inu.
Mundichitire chifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine. Mundichize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga.
Mundichiritse ine, Yehova, ndipo ndidzachiritsidwa; mundipulumutse ine, ndipo ndidzapulumutsidwa; pakuti chilemekezo changa ndinu.
Pakuti ndidzakubwezera iwe moyo, ndipo ndidzapoletsa mabala ako, ati Yehova; chifukwa anatcha iwe wopirikitsidwa, nati, Ndiye Ziyoni, amene kulibe munthu amfuna.
Taonani, ndidzautengera moyo ndi kuuchiritsa, ndi kuwachiritsa; ndipo ndidzawaululira iwo kuchuluka kwa mtendere ndi zoona.
Kodi mulibe vunguti mu Giliyadi? Kodi mulibe sing'anga m'menemo; analekeranji kuchira mwana wamkazi wa anthu anga?
Ndipo pamene Yesu anamva ichi, ananena nao, Akulimba safuna sing'anga, koma odwala ndiwo; sindinadza kudzaitana olungama, koma ochimwa.
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Amene ali olimba safuna sing'anga; koma akudwala ndiwo.
Ndipo mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, amene adasudzula asing'anga za moyo wake zonse, ndipo sanathe kuchiritsidwa ndi mmodzi yense,
Koma unyinji wa anthu, pamene anadziwa, anamtsata Iye; ndipo Iye anawalandira, nalankhula nao za Ufumu wa Mulungu, nachiritsa amene anasowa kuchiritsidwa.