Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 8:22 - Buku Lopatulika

22 Kodi mulibe vunguti mu Giliyadi? Kodi mulibe sing'anga m'menemo; analekeranji kuchira mwana wamkazi wa anthu anga?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Kodi mulibe vunguti m'Giliyadi? Kodi mulibe sing'anga m'menemo; analekeranji kuchira mwana wamkazi wa anthu anga?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Kodi ku Giliyadi kulibe mankhwala ochiritsa? Kodi kumeneko kulibe sing'anga? Chifukwa chiyani mabala a anthu anga sadapole?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Kodi ku Giliyadi kulibe mankhwala ochiritsa? Kodi kumeneko kulibe singʼanga? Nanga chifukwa chiyani mabala a anthu anga sanapole?

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 8:22
17 Mawu Ofanana  

Ndipo iwo anakhala pansi kuti adye chakudya; ndipo anatukula maso ao, nayang'ana, ndipo taonani, ulendo wa Aismaele anachokera ku Giliyadi ndi ngamira zao, zilinkunyamula zonunkhira ndi mafuta amankhwala ndi mure alinkumuka kutsikira nazo ku Ejipito.


Ndipo Israele atate wao anati kwa iwo, Ngati chomwecho tsopano chitani ichi: tengani zipatso za m'dziko muno m'zotengera zanu, mumtengere munthu uja mphatso, mafuta amankhwala pang'ono, ndi uchi pang'ono, zonunkhira ndi mure, ndi mfula, ndi katungurume;


Kodi mwakanadi Yuda? Kodi mtima wanu wanyansidwa ndi Ziyoni? Bwanji mwatipanda ife, ndipo tilibe kuchira? Tinayembekeza mtendere, koma sizinafike zabwino; tinayembekeza nthawi yakuchira, ndipo taonani mantha!


Pakuti Yehova atero za nyumba ya mfumu ya Yuda: Ndikuyesa iwe Giliyadi, ndi mutu wa Lebanoni; koma ndidzakuyesa iwe chipululu, ndi mizinda yosakhalamo anthu.


Kwera ku Giliyadi, tenga vunguti, namwali iwe mwana wa Ejipito; wachulukitsa mankhwala chabe; palibe kuchira kwako.


Babiloni wagwa dzidzidzi naonongedwa; mumkuwire iye; mutengere zowawa zake vunguti, kapena angachire.


Monga kasupe atulutsa madzi ake, chomwecho atulutsa zoipa zake; chiwawa ndi kufunkha zimveka m'kati mwake; pamaso panga masiku onse pali kulira ndi mabala.


Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!


Ndipo ndidzayesa Yerusalemu miyulu, mbuto ya ankhandwe; ndipo ndidzayesa mizinda ya Yuda bwinja, lopanda wokhalamo.


Ndikuchitire umboni wotani? Ndikuyerekeze ndi chiyani, mwana wamkazi wa Yerusalemu? Ndikulinganize ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwaliwe, mwana wamkazi wa Ziyoni? Popeza akula ngati nyanja; ndani angakuchize?


Yuda ndi dziko la Israele anagulana nawe malonda, anagula malonda ako ndi tirigu wa ku Miniti, ndi zozuna, ndi uchi, ndi mafuta, ndi mafuta amankhwala.


Koma ana a Rubeni ndi ana Gadi anali nazo zoweta zambirimbiri; ndipo anapenyerera dziko la Yazere, ndi dziko la Giliyadi, ndipo taonani, malowo ndiwo malo a zoweta.


Ndipo mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, amene adasudzula asing'anga za moyo wake zonse, ndipo sanathe kuchiritsidwa ndi mmodzi yense,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa