Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 9:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo Afarisi, pakuona ichi, ananena kwa ophunzira ake, Chifukwa ninji Mphunzitsi wanu alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo Afarisi, pakuona ichi, ananena kwa ophunzira ake, Chifukwa ninji Mphunzitsi wanu alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Pamene Afarisi adaona zimenezi, adafunsa ophunzira a Yesu kuti, “Bwanji aphunzitsi anu akudya pamodzi ndi okhometsa msonkho ndiponso ndi anthu ochimwa?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Ndipo Afarisi poona izi, anati kwa ophunzira ake, “Nʼchifukwa chiyani Aphunzitsi anu akudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 9:11
14 Mawu Ofanana  

amene ati, Ima pa wekha, usadze chifupi ndi ine, pakuti ine ndili woyera kupambana iwe; amenewa ndiwo utsi m'mphuno mwanga, moto woyaka tsiku lonse.


Mwana wa Munthu anadza wakudya, ndi wakumwa, ndipo iwo amati, Onani munthu wakudyaidya ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa! Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.


Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho?


Ndipo panali pamene Iye analinkukhala pachakudya m'nyumba, onani, amisonkho ndi ochimwa ambiri anadza nakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake.


Ndipo alembi a kwa Afarisi, pakuona kuti alinkudya nao ochimwa ndi amisonkho, ananena ndi ophunzira ake, Uyu akudya ndi kumwa nao amisonkho ndi ochimwa.


Ndipo m'mene anachiona anadandaula onse, nanena, Analowa amchereze munthu ali wochimwa.


Ndipo Afarisi ndi alembi ao anang'ung'udza kwa ophunzira ake, nanena, kuti, Bwanji inu mukudya ndi kumwa pamodzi ndi anthu amisonkho ndi ochimwa?


nanena kuti, Munalowa kwa anthu osadulidwa, ndi kudya nao.


Ife ndife Ayuda pachibadwidwe, ndipo sitili ochimwa a kwa amitundu;


akhale wokhoza kumva chifundo ndi osadziwa ndi olakwa, popeza iye yekhanso amazingwa ndi chifooko;


Munthu akadza kwa inu, wosatenga chiphunzitso ichi, musamlandire iye kunyumba, ndipo musampatse moni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa