ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.
Mateyu 8:11 - Buku Lopatulika Ndipo ndinena ndi inu, kuti ambiri a kum'mawa ndi a kumadzulo adzafika, nadzakhala pamodzi ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, mu Ufumu wa Kumwamba; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndinena ndi inu, kuti ambiri a kum'mawa ndi a kumadzulo adzafika, nadzakhala pamodzi ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, mu Ufumu wa Kumwamba; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndithu ndikunenetsa kuti ambiri adzabwera kuchokera kuvuma ndi kuzambwe nadzakhala nao pa phwando mu Ufumu wakumwamba pamodzi ndi Abrahamu, Isaki ndi Yakobe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikuwuzani kuti ambiri adzabwera kuchokera kummawa ndi kumadzulo, nadzakhala nawo pa phwando pamodzi ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo mu ufumu wakumwamba. |
ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.
mbeu zako zidzakhala monga fumbi lapansi, ndipo udzabalalikira kumadzulo ndi kum'mawa ndi kumpoto ndi kumwera: mwa iwe ndi mu mbeu zako mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa.
Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.
Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Yehova, ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.
Anakumbukira chifundo chake ndi chikhulupiriko chake kunyumba ya Israele; malekezero onse a dziko lapansi anaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Yese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu, amitundu adzafunafuna uwu; ndipo popuma pake padzakhala ulemerero.
Taonani, awa adzachokera kutali; ndipo taonani, awa ochokera kumpoto, ndi kumadzulo; ndi awa ochokera kudziko la Asuwani.
inde, ati, Chili chinthu chopepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israele; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale chipulumutso changa mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
Yehova wavula mkono wake woyera pamaso pa amitundu onse; ndi malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Chomwecho iwo adzaopa dzina la Yehova kuchokera kumadzulo, ndi ulemerero wake kumene kutulukira dzuwa; pakuti pamene mdani adzafika ngati chigumula, mzimu wa Yehova udzamkwezera mbendera yomletsa.
Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira cholowa cha bodza lokha, zopanda pake ndi zinthu zosapindula nazo.
Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka kunthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse, nudzakhala chikhalire.
Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.
Iwo ananena kwa Iye, Adzaononga koipa oipawo, nadzapereka mundawo kwa olima ena, amene adzambwezera iye zipatso pa nyengo zake.
Ndipo Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kumphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena.
Ndipo pakumva ichi, Yesu anazizwa, nati kwa iwo akumtsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israele, sindinapeze chikhulupiriro chotere.
Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m'chuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.
Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka kuchifuwa cha Abrahamu; ndipo mwini chumayo adafanso, naikidwa m'manda.
Ndipo anadabwa okhulupirirawo akumdulidwe onse amene anadza ndi Petro, chifukwa pa amitundunso panathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera.
Ndipo pamene anamva izi, anakhala duu, nalemekeza Mulungu, ndi kunena, Potero Mulungu anapatsa kwa amitundunso kutembenukira mtima kumoyo.
nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m'chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.
Pamene anafika nasonkhanitsa Mpingo anabwerezanso zomwe Mulungu anachita nao, kuti anatsegulira amitundu pa khomo la chikhulupiriro.
Kapena simudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna,
kuti amitundu ali olowa nyumba pamodzi ndi ife, ndi ziwalo zinzathu za thupilo, ndi olandira nafe pamodzi palonjezano mwa Khristu Yesu, mwa Uthenga Wabwino,
pamene palibe Mgriki ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Msukuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m'zonse.
ndicho chitsimikizo cha chiweruziro cholungama cha Mulungu; kuti mukawerengedwe oyenera ufumu wa Mulungu, umenenso mumvera zowawa;
Mwa fuko la Asere zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Nafutali zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Manase zikwi khumi ndi ziwiri.