Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 8:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo pakumva ichi, Yesu anazizwa, nati kwa iwo akumtsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israele, sindinapeze chikhulupiriro chotere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo pakumva ichi, Yesu anazizwa, nati kwa iwo akumtsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israele, sindinapeza chikhulupiriro chotere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Yesu atamva zimenezi, adachita chidwi, ndipo adauza anthu amene ankamutsata aja kuti, “Kunena zoona, ngakhale pakati pa Aisraele sindidapeze chikhulupiriro chotere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Yesu atamva zimenezi, anadabwa ndipo anati kwa omutsatira, “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti sindinapeze wina aliyense mu Israeli wachikhulupiriro chachikulu chotere.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 8:10
9 Mawu Ofanana  

Ndipo anakhala pamaso pake, woyamba monga ukulu wake, ndi wamng'ono monga ung'ono wake; ndipo anazizwa wina ndi wina.


Pomwepo Yesu anayankha, nati kwa iye, Mkaziwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu; chikhale kwa iwe monga momwe wafunira. Ndipo mwana wake anachira nthawi yomweyo.


Ndipo ndinena ndi inu, kuti ambiri a kum'mawa ndi a kumadzulo adzafika, nadzakhala pamodzi ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, mu Ufumu wa Kumwamba;


Pakuti inenso ndili munthu wakumvera ulamuliro, ndili nao asilikali akundimvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndi kwa kapolo wanga, Chita ichi, nachita.


Ndipo anazizwa chifukwa cha kusakhulupirira kwao. Ndipo anayendayenda m'midzi yozungulirapo, naphunzitsa.


Ndipo Iye, pakuona chikhulupiriro chao, anati, Munthu iwe, machimo ako akhululukidwa.


Ndipo Iye anati kwa mkaziyo, Chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.


Koma Yesu pakumva zimenezo anazizwa naye, napotolokera kwa anthu a mpingo wakumtsata Iye, nati, Ndinena kwa inu, sindinapeze, ngakhale mwa Israele, chikhulupiriro chachikulu chotere.


Ndipo anadabwa onse, nazizwa, nanena, Taonani, awa onse alankhulawa sali Agalileya kodi?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa