Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti,
Mateyu 4:14 - Buku Lopatulika kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zidaatero kuti zipherezere zimene mneneri Yesaya adaanena kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero pokwaniritsa zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yesaya kuti, |
Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti,
nakhalabe kumeneko kufikira atamwalira Herode; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri kuti, Ndinaitana Mwana wanga atuluke mu Ejipito.
nadza nakhazikika m'mzinda dzina lake Nazarete kuti chikachitidwe chonenedwa ndi aneneri kuti, Adzatchedwa Mnazarayo.
Koma izi zonse zinachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa.
ndipo anachoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye mu Kapernao wa pambali pa nyanja, m'malire a Zebuloni ndi Nafutali:
Dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali, njira ya kunyanja, kutsidya lija la Yordani, Galileya wa anthu akunja,
kotero kuti chikwaniridwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti, Iye yekha anatenga zofooka zathu, nanyamula nthenda zathu.
Pakuti ndinena ndi inu, chimene chidalembedwa chiyenera kukwanitsidwa mwa Ine, Ndipo anawerengedwa ndi anthu opanda lamulo; pakuti izi za kwa Ine zili nacho chimaliziro.
Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo.
Koma chitero, kuti mau olembedwa m'chilamulo chao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda chifukwa.
Chitapita ichi Yesu, podziwa kuti zonse zidatha pomwepo kuti lembo likwaniridwe, ananena, Ndimva ludzu.