Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 2:15 - Buku Lopatulika

15 nakhalabe kumeneko kufikira atamwalira Herode; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri kuti, Ndinaitana Mwana wanga atuluke mu Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 nakhalabe kumeneko kufikira atamwalira Herode; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri kuti, Ndinaitana Mwana wanga atuluke m'Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Adakhala kumeneko mpaka Herode atamwalira, kuti zipherezere zimene Ambuye adaalankhulitsa mneneri kuti, “Ndidaitana Mwana wanga kuti atuluke ku Ejipito.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 nakhala kumeneko mpaka Herode atamwalira. Ndipo zinakwaniritsidwa zomwe ananena Ambuye mwa mneneri kuti, “Ndinayitana mwana wanga kuti atuluke mu Igupto.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 2:15
21 Mawu Ofanana  

Pamenepo ukanene ndi Farao, Atero Yehova Mwana wanga, mwana wanga woyamba ndiye Israele.


Pamene Israele anali mwana, ndinamkonda, ndinaitana mwana wanga ali mu Ejipito.


Mulungu amtulutsa mu Ejipito; ali nayo mphamvu yonga ya njati; adzawadya amitundu, ndiwo adani ake. Nadzamphwanya mafupa ao, ndi kuwapyoza ndi mivi yake.


Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti,


Ndipo iye ananyamuka natenga kamwana ndi amake usiku, nachoka kupita ku Ejipito;


Pomwepo chinachitidwa chonenedwa ndi Yeremiya mneneri, kuti,


Koma pakumwalira Herode, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera m'kulota kwa Yosefe mu Ejipito,


nadza nakhazikika m'mzinda dzina lake Nazarete kuti chikachitidwe chonenedwa ndi aneneri kuti, Adzatchedwa Mnazarayo.


Ndipo ichi chinatero, kuti chikachitidwe chonenedwa ndi mneneri kuti,


Koma pakutero malembo adzakwaniridwa bwanji, pakuti kuyenera chomwecho?


Koma izi zonse zinachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa.


Ndipo pamene anampachika Iye, anagawana zovala zake ndi kulota maere:


kotero kuti chikwaniridwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti, Iye yekha anatenga zofooka zathu, nanyamula nthenda zathu.


Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo.


Chitapita ichi Yesu, podziwa kuti zonse zidatha pomwepo kuti lembo likwaniridwe, ananena, Ndimva ludzu.


Pakuti izi zinachitika, kuti lembo likwaniridwe, Fupa la Iye silidzathyoledwa.


Amuna inu, abale, kunayenera kuti lemba likwanitsidwe, limene Mzimu Woyera anayamba kunena mwa m'kamwa mwa Davide za Yudasi, wokhala mtsogoleri wa iwo adagwira Yesu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa