Mateyu 2:16 - Buku Lopatulika16 Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta mu Betelehemu ndi ta m'midzi yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta m'Betelehemu ndi ta m'milaga yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Herode atazindikira kuti akatswiri a nyenyezi aja adampusitsa, adatuma anthu ku Betelehemu ndi ku midzi yonse yozungulira, kuti akaphe ana aamuna onse a zaka ziŵiri kapena kucheperapo. Zaka zimenezi adaaŵerengera potsata m'mene adaamvera kwa akatswiri aja za nthaŵi imene iwowo adaaiwonera nyenyeziyo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Herode atazindikira kuti Anzeruwo anamupusitsa, anakwiya kwambiri. Ndipo anatumiza anthu kukapha ana onse aamuna a mʼBetelehemu ndi midzi yozungulira amene anali a zaka ziwiri kapena zocheperapo, molingana ndi nthawi imene Anzeruwo anamuwuza. Onani mutuwo |