Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 4:13 - Buku Lopatulika

13 ndipo anachoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye mu Kapernao wa pambali pa nyanja, m'malire a Zebuloni ndi Nafutali:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 ndipo anachoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye m'Kapernao wa pambali pa nyanja, m'malire a Zebuloni ndi Nafutali:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Adachokako ku Nazarete, nakakhala ku Kapernao, mzinda wina wa m'mbali mwa nyanja ku dera la Zebuloni ndi Nafutali.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ndipo atachoka ku Nazareti anapita ku Kaperenawo ndi kukhala mʼmbali mwa nyanja, mʼdera la Zebuloni ndi Nafutali;

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 4:13
17 Mawu Ofanana  

Ndipo iwe, Kapernao, udzakwezedwa kodi kufikira kuthambo? Udzatsika kufikira ku dziko la akufa! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa iwe zikadachitidwa mu Sodomu, uyo ukadakhala kufikira lero.


Ndipo pofika ku Kapernao amene aja akulandira ndalama za ku Kachisi anadza kwa Petro nati, Kodi Mphunzitsi wanu sapereka rupiyalo?


kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti,


Dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali, njira ya kunyanja, kutsidya lija la Yordani, Galileya wa anthu akunja,


Ndipo Iye analowa m'ngalawa, naoloka, nadza kumzinda kwao.


Ndipo iwo analowa mu Kapernao; ndipo pomwepo pa tsiku la Sabata iye analowa m'sunagoge naphunzitsa.


Ndipo polowanso Iye mu Kapernao atapita masiku ena, kunamveka kuti ali m'nyumba.


Ndipo iwe, Kapernao, kodi udzakwezedwa kufikira Kumwamba? Udzatsitsidwa kufikira ku dziko la akufa.


Ndipo anati kwa iwo, Kwenikweni mudzati kwa Ine nkhani iyi, Sing'anga iwe, tadzichiritsa wekha: zonse zija tazimva zinachitidwa ku Kapernao, muzichitenso zomwezo kwanu kuno.


Zitapita izi anatsikira ku Kapernao, Iye ndi amake, ndi abale ake, ndi ophunzira ake; nakhala komweko masiku owerengeka.


Chifukwa chake Yesu anadzanso ku Kana wa mu Galileya, kumene anasandutsa madzi vinyo. Ndipo kunali mkulu wina wa mfumu, mwana wake anadwala mu Kapernao.


ndipo pamene adalowa m'ngalawa, analikuoloka nyanja kunka ku Kapernao. Ndipo kutada pamenepo, koma Yesu asanadze kwa iwo.


chifukwa chake pamene khamu la anthu linaona kuti palibe Yesu, ndi ophunzira ake palibe, iwo okha analowa m'ngalawazo nadza ku Kapernao, alikufuna Yesu.


Izi ananena m'sunagoge, pakuphunzitsa mu Kapernao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa