Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.
Mateyu 19:8 - Buku Lopatulika Iye ananena kwa iwo, Chifukwa cha kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kuchotsa akazi anu; koma pachiyambi sikunakhala chomwecho. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iye ananena kwa iwo, Chifukwa cha kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kuchotsa akazi anu; koma pachiyambi sikunakhala chomwecho. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adaŵayankha kuti, “Mose adaakulolani kusudzula akazi anu chifukwa cha kukanika kwanuku. Komatu pa chiyambi sizinali choncho ai. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anayankha kuti, “Mose anakulolezani kuti muzisudzula akazi anu chifukwa cha kuwuma mitima kwanu. Koma sizinali chotere kuyambira pachiyambi. |
Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.
Ndipo analowa Nowa ndi ana ake ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake m'chingalawamo, chifukwa cha madzi a chigumula.
Yehova atero, Imani m'njira ndi kuona, funsani za mayendedwe akale, m'menemo muli njira yabwino, muyende m'menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu; koma anati, Sitidzayendamo.
Inde, anasanduliza mitima yao ikhale ngati mwala woti gwaa, kuti angamve chilamulo, ndi mau amene Yehova wa makamu anatumiza ndi Mzimu wake mwa aneneri oyamba aja; m'menemo munafuma mkwiyo waukulu wochokera kwa Yehova wa makamu.
Iwo ananena kwa Iye, Nanga chifukwa ninji Mose analamula kupatsa kalata yachilekaniro, ndi kumchotsa?
Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo: ndipo iye amene akwatira wochotsedwayo, achita chigololo.
Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye.
Ndipo mizimuyo inampempha Iye ninena, Ngati mutitulutsa, mutitumize ife tilowe m'gulu la nkhumbazo.
Ndipo chitatha icho anaonekera kwa khumi ndi mmodzi iwo okha, alikuseama pachakudya; ndipo anawadzudzula chifukwa cha kusavomereza kwao ndi kuuma mtima, popeza sanavomereze iwo amene adamuona, atauka Iye.