Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 16:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo chitatha icho anaonekera kwa khumi ndi mmodzi iwo okha, alikuseama pachakudya; ndipo anawadzudzula chifukwa cha kusavomereza kwao ndi kuuma mtima, popeza sanavomereze iwo amene adamuona, atauka Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo chitatha icho anaonekera kwa khumi ndi mmodzi iwo okha, alikuseama pachakudya; ndipo anawadzudzula chifukwa cha kusavomereza kwao ndi kuuma mtima, popeza sanavomereza iwo amene adamuona, atauka Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Potsiriza Yesu adaonekera ophunzira khumi ndi mmodzi aja alikudya. Adaŵadzudzula chifukwa cha kusakhulupirira kwao ndi kupulupudza kwao, chifukwa sadakhulupirire anzao aja amene adaamuwona Iye atauka kwa akufa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Pambuyo pake Yesu anaonekera kwa khumi ndi mmodziwo pamene ankadya; anawadzudzula chifukwa chopanda chikhulupiriro ndi kukanitsitsa kwawo kuti akhulupirire amene anamuona Iye atauka.

Onani mutuwo Koperani




Marko 16:14
24 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anati kwa Mose, Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, chinkana zizindikiro zonse ndinazichita pakati pao?


Pomwepo Iye anayamba kutonza mizindayo, m'mene zinachitidwa zambiri za ntchito zamphamvu zake, chifukwa kuti siinatembenuke.


Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakukanikani.


Ndipo pamene anamuona Iye, anamlambira; koma ena anakayika.


Ndipo ananena nao, Mutero inunso opanda nzeru kodi? Kodi simuzindikira kuti kanthu kalikonse kochokera kunja kukalowa mwa munthu, sikangathe kumdetsa iye;


Ndipo mau awa anaoneka pamaso pao ngati nkhani zachabe, ndipo sanamvere akaziwo.


Ndipo Iye anati kwa iwo, Opusa inu, ndi ozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri!


Chifukwa chake ophunzira ena ananena naye, Tamuona Ambuye. Koma iye anati kwa iwo, Ndikapanda kuona m'manja ake chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika chala changa m'chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika dzanja langa kunthiti yake; sindidzakhulupirira.


Ndipo pakupita masiku asanu ndi atatu ophunzira ake analinso m'nyumbamo, ndi Tomasi pamodzi nao. Yesu anadza, makomo ali chitsekere, naimirira pakati, nati, Mtendere ukhale ndi inu.


Pomwepo ananena kwa Tomasi, Bwera nacho chala chako kuno, nuone manja anga, ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliike kunthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupirira, koma wokhulupirira.


Zitapita izi Yesu anadzionetseranso kwa ophunzira ake kunyanja ya Tiberiasi. Koma anadzionetsera chotere.


Imeneyo ndi nthawi yachitatu yakudzionetsera Yesu kwa ophunzira ake, m'mene atauka kwa akufa.


kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zake, naonekera kwa iwo masiku makumi anai, ndi kunena zinthu za Ufumu wa Mulungu;


ndi kuti anaonekera kwa Kefa; pamenepo kwa khumi ndi awiriwo;


Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa