Usalankhule mwanthuku mtima wako, usafulumire kunena kanthu pamaso pa Mulungu; pakuti Mulungu ali kumwamba, iwe uli pansi; chifukwa chake mau ako akhale owerengeka.
Mateyu 14:9 - Buku Lopatulika Ndipo mfumuyo anagwidwa ndi chisoni; koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo anali naye pachakudya, analamulira upatsidwe; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumuyo anagwidwa ndi chisoni; koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo anali naye pachakudya, analamulira upatsidwe; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo mfumu Herode adamva chisoni. Koma chifukwa cha malumbiro ake ndiponso chifukwa cha anthu oitanidwa ku phwando aja, adalamula kuti ampatse mutu adaapemphawo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumuyo inamva chisoni koma chifukwa cha lumbiro lake ndi alendo amene anali pa phwando lake analamulira kuti chofuna chake chipatsidwe; |
Usalankhule mwanthuku mtima wako, usafulumire kunena kanthu pamaso pa Mulungu; pakuti Mulungu ali kumwamba, iwe uli pansi; chifukwa chake mau ako akhale owerengeka.
Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Inu ndi akazi anu mwanena ndi m'kamwa mwanu, ndi kukwaniritsa ndi manja anu kuti, Tidzachita ndithu zowinda zathu taziwindira, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira; khazikitsanitu zowinda zanu, chitani zowinda zanu.
Ndipo iye, atampangira amake, anati, Ndipatseni ine kuno m'mbale mutu wa Yohane Mbatizi.
Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lake lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo chifukwa chake mphamvu izi zichitachita mwa Iye.
pakuti Herode anaopa Yohane, podziwa kuti ali munthu wolungama ndi woyera mtima, ndipo anamsunga iye. Ndipo pamene anamva iye anathedwa nzeru, nakondwa kumva iye.
Ndipo mfumu inamva chisoni chachikulu; koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo akukhala pachakudya, sanafune kumkaniza.
Ndipo Iye anati kwa iwo, Pitani kauzeni nkhandweyo, Taonani, nditulutsa ziwanda, nditsiriza machiritso lero ndi mawa, ndipo mkucha nditsirizidwa.
Ndipo kunali pakutha miyezi iwiri, anabwerera kwa atate wake amene anamchitira monga mwa chowinda chake anachiwinda; ndipo sanamdziwe mwamuna. Motero unali mwambo mu Israele,
Koma amuna a Israele adalumbira ku Mizipa, ndi kuti, Palibe mmodzi wa ife adzapereka mwana wake wamkazi kwa Mbenjamini akhale mkazi wake.
Ndipo Aisraele anasauka tsiku lija; pakuti Saulo anawalumbirira, kuti, Atembereredwe iye wakudya kanthu kufikira madzulo, ndikabwezere chilango adani anga. Motero anthu onse anakhala opanda kudya.
Ndipo wina wa anthuwo anayankha, nati, Atate wanu analangiza anthu kolimba ndi lumbiro, ndi kuti, Wotembereredwa iye wakudya lero chakudya. Ndipo anthuwo analema.
Mulungu alange adani a Davide, ndi kuonjezerapo, ngati ndisiyapo kufikira kuunika kwa m'mawa, kanthu konse ka iye, kangakhale kamwana kamphongo.
Ndipo Saulo anamlumbirira kwa Yehova, nati, Pali Yehova, palibe chilango chidzakugwera chifukwa cha chinthu ichi.