Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 6:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lake lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo chifukwa chake mphamvu izi zichitachita mwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lake lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo chifukwa chake mphamvu izi zichitachita mwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Mfumu Herode adaazimva zimenezi, pakuti mbiri ya Yesu inali itamveka ponseponse. Anthu ena ankati, “Yohane Mbatizi uja adauka kwa akufa, nkuwona akuchita zamphamvu zonsezi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Mfumu Herode anamva zimenezi, pakuti dzina la Yesu linali litadziwika kwambiri. Ena amati, “Yohane Mʼbatizi waukitsidwa kwa akufa, ndipo nʼchifukwa chake mphamvu zochita zodabwitsa zinkagwira ntchito mwa Iye.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 6:14
16 Mawu Ofanana  

Napanga mu Yerusalemu makina, opangidwa ndi eni luso, akhale pansanja ndi kungodya, aponye nao mivi ndi miyala yaikulu. Ndi dzina lake linamveka kutali; pakuti anathandizidwa modabwitsa, mpaka analimbikatu.


Ndipo Aamoni anampatsa Uziya mitulo; ndi dzina lake linabuka mpaka polowera ku Ejipito; pakuti analimbika chilimbikire.


Koma iwo anatulukamo, nabukitsa mbiri yake m'dziko lonselo.


Ndipo mbiri yake inabuka pompaja kudziko lonse la Galileya lozungulirapo.


Koma iye anatuluka nayamba kulalikira ndithu, ndi kubukitsa mauwo, kotero kuti Yesu sanathe kulowanso poyera m'mudzi, koma anakhala padera m'mapululu; ndipo anadza kwa Iye anthu a kumalo onse.


Ndipo ananena, nati, Yohane Mbatizi; ndi ena, Eliya; koma ena, Mmodzi wa aneneri.


Nthawi yomweyo anadzapo Afarisi ena, nanena kwa Iye, Tulukani, chokani kuno; chifukwa Herode afuna kupha Inu.


Ndipo pa chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio Kaisara, pokhala Pontio Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode chiwanga cha Galileya, ndi Filipo mbale wake chiwanga cha dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lisaniasi chiwanga cha Abilene;


Ndipo mbiri yake imeneyo inabuka ku Yudeya yense, ndi ku dziko lonse loyandikira.


Ndipo anayankha nati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndi ena, kuti anauka mmodzi wa aneneri akale.


Pakuti kutuluka kwa inu kudamveka mau a Ambuye, osati mu Masedoniya ndi Akaya mokha, komatu m'malo monse chikhulupiriro chanu cha kwa Mulungu chidatuluka; kotero kuti sikufunika kwa ife kulankhula kanthu.


pochita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa