Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 14:24 - Buku Lopatulika

24 Ndipo Aisraele anasauka tsiku lija; pakuti Saulo anawalumbirira, kuti, Atembereredwe iye wakudya kanthu kufikira madzulo, ndikabwezere chilango adani anga. Motero anthu onse anakhala opanda kudya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ndipo Aisraele anasauka tsiku lija; pakuti Saulo anawalumbirira, kuti, Atembereredwe iye wakudya kanthu kufikira madzulo, ndikabwezere chilango adani anga. Motero anthu onse anakhala opanda kudya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Koma ankhondo a Aisraele adavutika tsiku limene lija, pakuti Saulo adaŵaopseza pakunena kuti, “Atembereredwe amene adye kanthu kusanade, ndisanalipsire adani anga.” Motero panalibe ndi mmodzi yemwe amene adalaŵa chakudya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Koma asilikali a Israeli anavutika tsiku limenelo, chifukwa Sauli anawalumbirira Aisraeli kuti, “Wotembereredwa munthu aliyense amene adzadya kusanade, ine ndisanalipsire adani anga!” Kotero palibe wankhondo aliyense amene analawa chakudya.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 14:24
19 Mawu Ofanana  

Ndiye Mulungu amene andibwezerera chilango, nandigonjetsera mitundu ya anthu.


Wonyoza Mulungu aononga mnzake ndi m'kamwa mwake; koma olungama adzapulumuka pakudziwa.


Asamuombole munthu woperekedwa chiperekere kwa Mulungu; amuphe ndithu.


kapena munthu akalumbira ndi milomo yake osalingirira kuchita choipa, kapena kuchita chabwino, chilichonse munthu akalumbira osalingirira, ndipo chidambisikira; koma pochizindikira akhala wopalamula chimodzi cha izi:


Ndipo Israele analonjeza chowinda kwa Yehova, nati, Mukadzaperekatu anthu awa m'dzanja langa, ndidzaononga mizinda yao konse.


pamenepo wansembe alumbiritse mkazi lumbiro lakutemberera, ndi wansembe anene kwa mkazi, Yehova akuike ukhale temberero ndi lumbiro pakati pa anthu a mtundu wako, pakuondetsa Yehova m'chuuno mwako, ndi kukutupitsa thupi lako;


Pakuti ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziwitso.


Ngati wina sakonda Ambuye, akhale wotembereredwa. Akudza Ambuye.


Ndipo Yoswa anawalumbirira nyengo ija, ndi kuti, Wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzauka ndi kumanga mzinda uwu wa Yeriko; adzamanga maziko ake ndi kutayapo mwana wake woyamba, nadzaimika zitseko zake ndi kutayapo mwana wake wotsirizira.


Ndipo kunali, atakula mphamvu Israele, anasonkhetsa Akanani, osawaingitsa onse.


Lemekezani Yehova pakuti atsogoleri mu Israele anatsogolera, pakuti anthu anadzipereka mwaufulu.


Ndipo anthu onsewo analowa munkhalango, panali uchi pansi.


Pakuti, pali Yehova wakupulumutsa Israele, chingakhale chili m'mwana wanga Yonatani, koma adzafa ndithu. Koma pakati pa anthu onse panalibe mmodzi wakumyankha iye.


Nati Saulo, Mudzatero kwa Davide, kuti mfumu safuna cholowolera china, koma nsonga za makungu zana limodzi za Afilisti, kuti abwezere chilango adani a mfumu. Koma Saulo anaganizira kupha Davide ndi dzanja la Afilisti.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa