Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 14:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo iye, atampangira amake, anati, Ndipatseni ine kuno m'mbale mutu wa Yohane Mbatizi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo iye, atampangira amake, anati, Ndipatseni ine kuno m'mbale mutu wa Yohane Mbatizi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Tsono mai wake atamuuza choti apemphe, mwana wamkazi uja adati, “Mundipatse pompano mutu wa Yohane Mbatizi m'mbale.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ndipo atamupangira amayi ake anati, “Mundipatse pomwe pano mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 14:8
17 Mawu Ofanana  

Kodi sanakuuzeni mbuye wanga chimene ndidachita m'kuwapha Yezebele aneneri a Yehova, kuti ine ndidabisa aneneri a Yehova zana limodzi makumi asanu asanu m'phanga, ndi kuwadyetsa mkate ndi madzi?


pakuti pamene Yezebele anapulula aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri zana limodzi, nawabisa makumi asanu asanu m'phanga, nawadyetsa mkate ndi madzi.


Tsono Yezebele anatuma mthenga kwa Eliya, wakuti, Milungu indilange nionjezepo, ngati sindilinganiza moyo wako ndi moyo wa mmodzi wa iwowo mawa nthawi yomwe ino.


Pamene Ataliya make wa Ahaziya anaona kuti mwana wake wafa, ananyamuka, naononga mbeu yonse yachifumu.


Kuwerenga kwake ndiko: mbale zagolide makumi atatu, mbale zasiliva chikwi chimodzi, mipeni makumi awiri mphambu isanu ndi inai;


pakuti mapazi ao athamangira zoipa, afulumira kukhetsa mwazi.


Anthu ankhanza ada wangwiro; koma oongoka mtima asamalira moyo wake.


chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake ndiko masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwirizo zodzala ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ukhale nsembe yaufa;


anabwera nacho chopereka chake mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosakaniza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;


Ndipo anautenga mutu wake m'mbalemo, naupatsa buthulo: ndipo iye anamuka nao kwa amake.


Pomwepo iye anamlonjeza chilumbirire, kumpatsa iye chimene chilichonse akapempha.


Ndipo mfumuyo anagwidwa ndi chisoni; koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo anali naye pachakudya, analamulira upatsidwe;


Ndipo anatuluka, nati kwa amake, Ndidzapempha chiyani? Ndipo iye anati, Mutu wake wa Yohane Mbatizi.


Ndipo pomwepo analowa m'mangum'mangu kwa mfumu, napempha kuti, Ndifuna kuti mundipatse tsopano apa, mutu wake wa Yohane Mbatizi mumbale.


natengera mutu wake mumbale, naupereka kwa buthulo; ndipo buthu linaupereka kwa amake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa