Atero Kirusi mfumu ya ku Persiya, Yehova Mulungu Wam'mwamba anandipatsa maufumu onse a padziko lapansi, nandilangiza ndimmangire nyumba mu Yerusalemu, ndiwo mu Yuda.
Masalimo 85:2 - Buku Lopatulika Munachotsa mphulupulu ya anthu anu, munafotsera zolakwa zao zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Munachotsa mphulupulu ya anthu anu, munafotsera zolakwa zao zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mudakhululukira machimo a anthu anu, mudafafaniza zolakwa zao zonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Munakhululukira mphulupulu za anthu anu ndi kuphimba machimo awo onse. Sela |
Atero Kirusi mfumu ya ku Persiya, Yehova Mulungu Wam'mwamba anandipatsa maufumu onse a padziko lapansi, nandilangiza ndimmangire nyumba mu Yerusalemu, ndiwo mu Yuda.
Koma Iye pokhala ngwa chifundo, anakhululukira choipa, osawaononga; nabweza mkwiyo wake kawirikawiri, sanautse ukali wake wonse.
Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, zoipa za Israele zidzafunidwa, koma zidzasoweka; ndi zochimwa za Yuda, koma sizidzapezeka; pakuti ndidzakhululukira iwo amene ndidzawasiya ngati chotsala.
Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.
Khululukiranitu mphulupulu ya anthu awa, monga mwa chifundo chanu chachikulu, ndi monga mudalekerera anthu awa, kuyambira Ejipito kufikira tsopano.
ndipo mwa Iye yense wokhulupirira ayesedwa wolungama kumchotsera zonse zimene simunangathe kudzichotsera poyesedwa wolungama ndi chilamulo cha Mose.
Ndipo inu, pokhala akufa m'zolakwa ndi kusadulidwa kwa thupi lanu, anakupatsani moyo pamodzi ndi Iye, m'mene adatikhululukira ife zolakwa zonse;