Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 1:2 - Buku Lopatulika

2 Atero Kirusi mfumu ya ku Persiya, Yehova Mulungu Wam'mwamba anandipatsa maufumu onse a padziko lapansi, nandilangiza ndimmangire nyumba mu Yerusalemu, ndiwo mu Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Atero Kirusi mfumu ya ku Persiya, Yehova Mulungu Wam'mwamba anandipatsa maufumu onse a pa dziko lapansi, nandilangiza ndimmangire nyumba m'Yerusalemu, ndiwo m'Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Kirusi, mfumu ya ku Persiya, akunena kuti, ‘Chauta, Mulungu Wakumwamba, wandipatsa ine maiko onse a pa dziko lonse lapansi, ndipo wandilamula kuti ndimmangire Nyumba ku Yerusalemu, ku dziko la Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Iye anati, “Koresi mfumu ya Perisiya ikunena kuti, “ ‘Yehova, Mulungu wakumwamba wandipatsa maufumu onse a dziko lapansi, ndipo wandipatsa udindo woti ndimumangire Nyumba ku Yerusalemu mʼdziko la Yuda.

Onani mutuwo Koperani




Ezara 1:2
34 Mawu Ofanana  

Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani, thambo ndi mu Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.


Huramu anatinso, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nampatsa mfumu Davide mwana waluso, wodziwa nzeru ndi waluntha, ammangire Yehova nyumba, ndiponso nyumba ya ufumu wake.


Pamenepo ananyamuka akulu a nyumba za makolo a Yuda ndi Benjamini, ndi ansembe, ndi Alevi, ndiwo onse amene Mulungu adawautsira mzimu wao akwere kukamanga nyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu.


Anaperekanso ndalama kwa amisiri a miyala, ndi a mitengo; ndi chakudya, ndi chakumwa, ndi mafuta, kwa a ku Sidoni, ndi a ku Tiro, kuti atenge mikungudza ku Lebanoni, kufika nayo ku nyanja ku Yopa, monga adawalola Kirusi mfumu ya Persiya.


Koma Zerubabele, ndi Yesuwa, ndi akulu otsala a nyumba za makolo a Israele, anati kwa iwo, Sikuyenera ndi inu ndi ife kumangira Mulungu wathu nyumba, koma ife tokha pamodzi tidzamangira Yehova Mulungu wa Israele, monga mfumu Kirusi mfumu ya Persiya watilamulira.


nati naye, Tenga zipangizo izi, kaziike mu Kachisi ali mu Yerusalemu, nimangidwe nyumba ya Mulungu pambuto pake.


kuti apereke nsembe zonunkhira bwino kwa Mulungu wa Kumwamba, napempherere moyo wa mfumu ndi wa ana ake.


Chaka choyamba cha Kirusi mfumu, analamulira Kirusi mfumuyo, Kunena za nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, imangidwe nyumbayi pamalo pophera nsembe, namangidwe kolimba maziko ake, msinkhu wake mikono makumi asanu ndi limodzi, kupingasa kwake mikono makumi asanu ndi limodzi;


Arita-kisereksesi mfumu ya mafumu kwa Ezara wansembe, mlembi wa lamulo la Mulungu wa Kumwamba, mtendere weniweni, ndi pa nthawi yakuti.


Ndipo kunali, pakumva mau awa, ndinakhala pansi ndi kulira misozi, ndi kuchita maliro masiku ena, ndinasalanso, ndi kupemphera pamaso pa Mulungu wa Kumwamba,


ndi kuti, Ndikupembedzani Yehova, Mulungu wa Kumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake;


Yamikani Mulungu wa Kumwamba, pakuti chifundo chake nchosatha.


Munachotsa mphulupulu ya anthu anu, munafotsera zolakwa zao zonse.


Mtima wa mfumu uli m'dzanja la Yehova ngati mitsinje ya madzi; aulozetsa komwe afuna.


Ndani anautsa wina wochokera kum'mawa, amene amuitana m'chilungamo, afike pa phazi lake? Iye apereka amitundu patsogolo pake, namlamuliritsa mafumu; nawapereka monga fumbi kulupanga lake, monga chiputu chouluzidwa ku uta wake.


Ndine amene ndilimbitsa mau a mtumiki wanga, kuchita uphungu wa amithenga anga; ndi kunena za Yerusalemu, Adzakhalamo anthu; ndi za mizinda ya Yuda; Idzamangidwa; ndipo ndidzautsa malo abwinja ake.


ndi kunena za Kirusi, Iye ndiye mbusa wanga, ndipo adzachita zofuna zanga zonse; ndi kunena za Yerusalemu, Adzamangidwa; ndi kwa Kachisi, Maziko ako adzaikidwa.


Atero Yehova kwa wodzozedwa wake kwa Kirusi, amene dzanja lake lamanja ndaligwiritsa, kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pake, ndipo ndidzamasula m'chuuno mwa mafumu; atsegule zitseko pamaso pake, ndi zipata sizidzatsekedwa:


Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?


Muzitero nao, milungu imene sinalenge miyamba ndi dziko lapansi, iyo idzatha kudziko lapansi, ndi pansi pa miyambayo.


Ine ndinalenga dziko lapansi, anthu ndi nyama zokhala m'dzikomo, ndi mphamvu yanga yaikulu ndi mkono wanga wotambasuka; ndipo ndinapereka ilo kwa iye amene ayenera pamaso panga.


Pakuti Yehova atero, kuti, Zitapita zaka makumi asanu ndi awiri pa Babiloni, ndidzakuyang'anirani inu, ndipo ndidzakuchitirani inu mau anga abwino, ndi kubwezera inu kumalo kuno.


Nakhala moyo Daniele mpaka chaka choyamba cha mfumu Kirusi.


pakuti amasanduliza nthawi ndi nyengo, achotsa mafumu, nalonga mafumu, apatsa anzeru nzeru, ndi chidziwitso kwa iwo okhoza kuzindikira.


koma kuli Mulungu Kumwamba wakuvumbulutsa zinsinsi; Iye ndiye wadziwitsa mfumu Nebukadinezara chimene chidzachitika masiku otsiriza. Loto lanu, ndi masomphenya a m'mtima mwanu pakama panu, ndi awa:


kuti adzakuingitsani kukuchotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng'ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, ndipo zidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.


Nadzakuinga kukuchotsa kwa anthu, ndi pokhala pako udzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo; adzakudyetsa udzu ngati ng'ombe; ndipo zidzakupitira nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka udzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.


koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yake kwa inu; ndi inu ndi akulu anu, akazi anu ndi akazi anu aang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitire ulemu.


Pamenepo mfumu Dariusi analembera kwa anthu, mitundu ya anthu, ndi a manenedwe onse okhala padziko lonse lapansi, Mtendere uchulukire inu.


Ndipo ananena nao, Ndine Muhebri, ndiopa Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene analenga nyanja ndi mtunda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa