Masalimo 71:8 - Buku Lopatulika M'kamwa mwanga mudzadzala lemekezo lanu, ndi ulemu wanu tsiku lonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 M'kamwa mwanga mudzadzala lemekezo lanu, ndi ulemu wanu tsiku lonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakamwa panga pakutamanda Inu, pakulalika ulemerero wanu tsiku lonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakamwa panga padzaza ndi matamando anu, kulengeza ulemerero wanu tsiku lonse. |
Ndidzalemekeza Yehova m'moyo mwanga; ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wanga pokhala ndi moyo ine.
Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona; ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakufuula mokondwera.
Pakamwa panga padzafotokozera chilungamo chanu, ndi chipulumutso chanu tsiku lonse; pakuti sindidziwa mawerengedwe ake.
Lilime langa lomwe lidzalankhula za chilungamo chanu tsiku lonse, pakuti ofuna kundichitira choipa achita manyazi, nadodoma.
Pamaso pake pali ulemu ndi ukulu. M'malo opatulika mwake muli mphamvu ndi zochititsa kaso.