Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 71:15 - Buku Lopatulika

15 Pakamwa panga padzafotokozera chilungamo chanu, ndi chipulumutso chanu tsiku lonse; pakuti sindidziwa mawerengedwe ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Pakamwa panga padzafotokozera chilungamo chanu, ndi chipulumutso chanu tsiku lonse; pakuti sindidziwa mawerengedwe ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Pakamwa panga padzalankhula tsiku lonse za ntchito zanu zolungama ndi za chipulumutso chanu, popeza kuti sindidziŵa chiŵerengero chake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Pakamwa panga padzafotokoza za chilungamo chanu, za chipulumutso chanu tsiku lonse, ngakhale sindikudziwa muyeso wake.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 71:15
18 Mawu Ofanana  

Muimbireni Yehova, inu dziko lonse lapansi, lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.


Masiku onse ndidzakuyamikani; ndi kulemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi.


kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse.


Ndipo lilime langa lilalikire chilungamo chanu, ndi lemekezo lanu tsiku lonse.


Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima.


Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziwerenga.


Nsembe ndi chopereka simukondwera nazo; mwanditsegula makutu. Nsembe yopsereza ndi yamachimo simunapemphe.


Pakuti simukondwera ndi nsembe, mwenzi nditapereka; nsembe yopsereza simuikonda.


Lilime langa lomwe lidzalankhula za chilungamo chanu tsiku lonse, pakuti ofuna kundichitira choipa achita manyazi, nadodoma.


M'kamwa mwanga mudzadzala lemekezo lanu, ndi ulemu wanu tsiku lonse.


Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu. Ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine, kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.


Akondwera m'dzina lanu tsiku lonse; ndipo akwezeka m'chilungamo chanu.


ukasunge zolingalira, milomo yako ilabadire zomwe udziwa.


Posamveka phokoso la amauta potunga madzi, pomwepo adzafotokozera zolungama anazichita Yehova, zolungama anazichita m'madera ake, mu Israele. Pamenepo anthu a Yehova anatsikira kuzipata.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa