Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 71:14 - Buku Lopatulika

14 Koma ine ndidzayembekeza kosaleka, ndipo ndidzaonjeza kukulemekezani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Koma ine ndidzayembekeza kosaleka, ndipo ndidzaonjeza kukulemekezani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Koma ine ndidzakhulupirira Inu nthaŵi zonse, ndipo ndidzapitirizabe kukutamandani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Koma ine ndidzakhala ndi chiyembekezo mwa Inu nthawi zonse, ndidzakutamandani mowirikizawirikiza.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 71:14
14 Mawu Ofanana  

Angakhale andipha koma ndidzamlindira; komanso ndidzaumirira mayendedwe anga pamaso pake.


Israele, uyembekezere Yehova; chifukwa kwa Yehova kuli chifundo, kwaonso kuchulukira chiombolo.


Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamyamikanso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga, ndi Mulungu wanga.


Inu munandigwiriziza kuyambira ndisanabadwe, kuyambira pa thupi la mai wanga wondichitira zokoma ndinu; ndidzakulemekezani kosalekeza.


Ndili nacho chiyembekezo popeza ndilingalira ichi ndiyembekeza kanthu.


Moyo wanga uti, Gawo langa ndiye Yehova; chifukwa chake ndidzakhulupirira.


Yehova akhalira wabwino omlindirira, ndi moyo womfunafuna.


Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha chipulumutso cha Yehova.


Ndipo ichi ndipempha, kuti chikondi chanu chisefukire chionjezere, m'chidziwitso, ndi kuzindikira konse;


pakutinso munawachitira ichi abale onse a mu Masedoniya yense. Koma tikudandaulirani, abale, muchulukireko koposa,


Potero musataye kulimbika kwanu, kumene kuli nacho chobwezera mphotho chachikulu.


Mwa ichi, podzimanga m'chuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga, nimuyembekeze konsekonse chisomo chilikutengedwa kudza nacho kwa inu m'vumbulutso la Yesu Khristu;


Koma kulani m'chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu; kwa Iye kukhale ulemerero, tsopano ndi nthawi zonse. Amen.


Ndipo yense wakukhala nacho chiyembekezo ichi pa Iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali Woyera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa