Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 71:13 - Buku Lopatulika

13 Adani a moyo wanga achite manyazi, nathawe; chotonza ndi chimpepulo zikute ondifunira choipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Adani a moyo wanga achite manyazi, nathawe; chotonza ndi chimpepulo zikute ondifunira choipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Anthu ondineneza achite manyazi ndipo aonongeke. Anthu ofunafuna kundipweteka anyozedwe, ndipo achite manyazi kotheratu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ondineneza anga awonongeke mwa manyazi, iwo amene akufuna kundipweteka avale chitonzo ndi manyazi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 71:13
12 Mawu Ofanana  

pakuti Ayuda anasonkhana pamodzi m'mizinda mwao, m'maiko onse a mfumu Ahasuwero, kuwathira manja ofuna kuwachitira choipa, ndipo palibe munthu analimbika pamaso pao; popeza kuopsa kwao kudawagwera mitundu yonse ya anthu.


Otsutsana nane avale manyazi, nadzikute nacho chisokonezo chao ngati ndi chofunda.


Ndidzawaveka adani ake ndi manyazi; koma pa iyeyu korona wake adzamveka.


Achite manyazi, nadodome iwo akukondwera chifukwa cha choipa chidandigwera. Avekeke ndi manyazi ndi kupunzika iwo akudzikuza pa ine.


Athe nzeru nachite manyazi iwo akufuna moyo wanga; abwezedwe m'mbuyo nasokonezeke iwo akundipangira chiwembu.


Adzachita manyazi, nadzanthunthumira kwakukulu adani anga onse; adzabwerera, nadzachita manyazi modzidzimuka.


Abwerere, kukhale mphotho ya manyazi ao amene akuti, Hede, hede.


Lilime langa lomwe lidzalankhula za chilungamo chanu tsiku lonse, pakuti ofuna kundichitira choipa achita manyazi, nadodoma.


Taona, onse amene akukwiyira iwe adzakhala ndi manyazi, nasokonezedwa; iwo amene akangana ndi iwe adzakhala ngati chabe, nadzaonongeka.


Koma Yehova ali ndi ine ngati wamphamvu ndi woopsa; chifukwa chake ondisautsa adzaphunthwa, sadzandilala; adzakhala ndi manyazi ambiri, chifukwa sanachite chanzeru, ngakhale ndi kunyazitsa kwamuyaya kumene sikudzaiwalika.


Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa