Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupemba kwanga; ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu.
Masalimo 71:2 - Buku Lopatulika Ndikwatuleni m'chilungamo chanu, ndi kundilanditsa, nditcherereni khutu lanu ndi kundipulumutsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndikwatuleni m'chilungamo chanu, ndi kundilanditsa, nditcherereni khutu lanu ndi kundipulumutsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma mundilanditse ndi kundipulumutsa, pakuti ndinu Mulungu wolungama. Tcherani khutu kuti mundimve, ndipo mundipulumutse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mundilanditse ndi kundipulumutsa mwa chilungamo chanu, mutchere khutu lanu ndi kundipulumutsa. |
Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupemba kwanga; ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu.
Mundipatse moyo, Yehova, chifukwa cha dzina lanu; mwa chilungamo chanu mutulutse moyo wanga m'sautso.
Ine ndinakuitanani, pakuti mudzandiyankha, Mulungu; tcherani khutu lanu kwa ine, imvani mau anga.
Ndakhulupirira Inu, Yehova, ndikhale wopanda manyazi nthawi zonse, mwa chilungamo chanu ndipulumutseni ine.
Munditcherere khutu lanu; ndipulumutseni msanga. Mundikhalire ine thanthwe lolimba, nyumba yamalinga yakundisunga.
Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda chifundo. Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama.
Ambuye, monga mwa chilungamo chanu chonse, mkwiyo wanu ndi ukali wanu zitembenuketu, zichoke kumzinda wanu Yerusalemu, phiri lanu lopatulika; pakuti mwa zochimwa zathu, ndi mphulupulu za makolo athu, Yerusalemu ndi anthu anu asanduka chotonza cha onse otizungulira.
Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.