Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?
Masalimo 67:4 - Buku Lopatulika Anthu akondwere, nafuule mokondwera; pakuti mudzaweruza anthu molunjika, ndipo mudzalangiza anthu padziko lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anthu akondwere, nafuule mokondwera; pakuti mudzaweruza anthu molunjika, ndipo mudzalangiza anthu pa dziko lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mitundu ya anthu isangalale ndi kuimba ndi chimwemwe, chifukwa Inu mumaweruza anthu mwachilungamo, ndi kuŵatsogolera pa dziko lapansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mitundu yonse ya anthu isangalale ndi kuyimba mwachimwemwe, pakuti inu mumaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo ndi kutsogolera mitundu ya anthu a dziko lapansi. |
Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?
Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale cholowa chako, ndi malekezero a dziko lapansi akhale akoako.
Nenani mwa amitundu, Yehova achita ufumu; dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke; adzaweruza mitundu ya anthu molunjika.
Pamaso pa Yehova, popeza akudza kudzaweruza dziko lapansi; adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndipo mitundu ya anthu molunjika.
Imba, iwe wouma, amene sunabale; imba zolimba ndi kufuula zolimba, iwe amene sunabale mwana; pakuti ana a mfedwa achuluka koposa ana a mkazi wokwatibwa ndi mwamuna, ati Yehova.
Gulu la ngamira lidzakukuta, ngamira zazing'ono za Midiyani ndi Efa; iwo onsewo adzachokera ku Sheba adzabwera nazo golide ndi lubani; ndipo adzalalikira matamando a Yehova.
chifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m'chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse chitsimikizo, pamene anamuukitsa Iye kwa akufa.
Koma kolingana ndi kuuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziunjikira wekha mkwiyo pa tsiku la mkwiyo ndi la kuvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu;
Pakuti kwalembedwa, Kondwera, chumba iwe wosabala; imba nthungululu, nufuule iwe wosamva kuwawa kwa kubala; pakuti ana ake a iye ali mbeta achuluka koposa ana a iye ali naye mwamuna.
Kondwerani, amitundu inu, ndi anthu ake; adzalipsira mwazi wa atumiki ake, adzabwezera chilango akumuukira, nadzafafanizira zoipa dziko lake, ndi anthu ake.