Masalimo 67:3 - Buku Lopatulika Anthu akuyamikeni, Mulungu; anthu onse akuyamikeni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anthu akuyamikeni, Mulungu; anthu onse akuyamikeni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu, mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu; mitundu yonse ya anthu ikutamandeni. |
Tulutsani moyo wanga m'ndende, kuti ndiyamike dzina lanu; olungama adzandizinga; pakuti mudzandichitira zokoma.
Ndidzawakumbutsa dzina lanu m'mibadwomibadwo; chifukwa chake mitundu ya anthu idzayamika Inu kunthawi za nthawi.
inde, ati, Chili chinthu chopepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israele; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale chipulumutso changa mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
Chifukwa chake Iye adzawapereka kufikira nthawi yoti wobalayo wabala; pamenepo otsala a abale ake adzabwera pamodzi ndi ana a Israele.